Nkhuku yomwa dzira lake lomwe ainjata

55

Apolisi ku Mangochi agwila Bambo wina wa zaka 40 kamba kogwilila ndi kupeleka mimba kwa mwana wake.

Malinga ndi onenela a Polisi mu boma la Mangochi, a Amina Daudi, Bambo amene watsekeledwayu kwawo ndi ku Mulanje.

Iwo ananena kuti Bambo ameneyo ndi mkazi wake banja linatha.

Iye ananyamuka kupita ku Mangochi kumene anakwatila mkazi wina. Ali kumeneko anaitanitsa mwana wake wamkazi kuti azikhala naye.

Apolisi akuti mu mwezi wa July chaka chatha cha 2016, mkazi wa tsopano wa bamboyu anachoka. Kumusiya mkuluyo ndi mwana wake. Mmbuyomu mkuluyo anakakamiza mwana wake kuchita naye zadama.

Mwana uja ati anathawila kwa Mayi ake omubeleka ku Mulanje kumene miyezi itapita anadziwika kuti ali ndi pakati. Atamufunsa anakanika kuulula kuti wanyamula katundu wa Bambo ake. Iwo anamuthamangitsa, kumuuza abwelele ku Mangochi.

Ku Mangochi, Bambo ake anamusungitsa kwa chibwenzi chawo kuti mkazi anakwatila uja asadziwe.

Koma anthu a mmudzi podabwa anamupana mtsikanayo amene anaulula kuti atate ake ndiwo anamuchimwitsa. Nkhani inakafika ku Polisi ndipo Bambo wadyelayu anagwidwa.

Mkuluyo akuyembekezeka kukayankha mlandu ogona ndi m’bale wake.

Share.

55 Comments

  1. Zimenezo sizachilendo,ku Nsanje kuno,bambo wina ali ndi ana ake anayi atsikana+nse anagonana nawo,wachinayi atagonana naye anapititsa nkhani ku Police,anamangidwa,khani inapita kubwalo la milandu(khoti)chikhalilecho mkazi wake ali naye koma mkaziyo amachita mantha kuti banja lingathe,Zomvetsa chisoni kuti bamboyo ali positive,just imagine,This is a true story,I know him and his daugthters too,its nor kukhwimila 4 him but he is stupid.

  2. Ine sinkuonapo mwana apa onsewa ndi akulu ndipo pofika kupatsana mimba sanayambe lero zangovuta kuti mwanayo ndiwake

  3. Bmbo zaka 40 mwana 21 ~~~~~ sanamugwilire panali chibwezi apa yamvuta ndi mimbayi pachikhalidwe cha achawa NYASIIIII»»»»»»»

  4. Nyele chani? Osakanyenga mahule bwanji? Kufunakukwima chani? Mbuzi yamuthu kodi akaziake alibe nyelo bwanji? Ngti alinayo osakanyenga mkazi wake bwanji? Unyakundende ukanyenga khomauziwona ble mwina umangova.

  5. Nyele chani? Osakanyenga mahule bwanji? Kufunakukwima chani? Mbuzi yamuthu kodi akaziake alibe nyelo bwanji? Ngti alinayo osakanyenga mkazi wake bwanji? Unyakundende ukanyenga khomauziwona ble mwina umangova.

  6. Musana postite nkhani muziyamba mwalemba ndikuiwelengaso nokha then ndikuposta osati nyasi mumaposta zagramalayi,chochobe poti munapeza mwayi ogwila ntchito kumeneko bola mukumalandila palibe vuto

%d bloggers like this: