Atatu atuluka super league, imodzi m’chigawo chilichonse

Advertisement
Karonga United

Matimu atatu omwe amasewera mu Tnm super league atuluka mu mpikisanowo omwe ndi waukulu m’dziko muno. Izi zatsimikizika kumathero a sabata latha.

Malawi24 itha kutsikimiza kuti matimu atatu, imodzi imodzi kuchokera muzigawo zikulu zikulu zamdziko muno aona msana wanjira zitawavuta mu ligi ya pamwambayi.

Karonga United
Karonga United nayonso yatuluka mumpikisanowu.

Zachitikazi zili zosiyana ndi chaka chatha pomwe matimu awiri ochokera mu chigawo chapakati pamene imodzi kuchokera m’chigawo chakumwera adaona msana wanjira.

Matimu omwe anatuluka chaka chatha kuchokera chigawo chapakati adali timu ya asilikali ya Airborne Rangers komanso Dedza Young soccer saints pamene yomwe inatuluka m’chigawo chakummwera idali team ya Wizards yomwe pano imatchuka ndi dzina loti Premier Bet Wizards.

Pamene chaka chino timu ya Civo United yochokera chigawo chapakati yatuluka mu league yaikulu ya m’dziko muno itasewera mu league ya super league kwa zaka zoposa khumi ndi zitatu (30). Civo idatsikimizidwa kuti yatuluka pomwe timuyi idagonja ndi chigoli chimodzi kwa duu ndi timu ya Nyasa Big Bullets yomwe ikuteteza chikhochi.

Pamene Karonga United kuchokera ku chigawo chakumpoto idatuluka itasinjidwa 2 kwa tetete ndi timu ya asilikali yochokera Ku Lilongwe ya Kamuzu Barracks yomwe ikutsogola pa liwiro lamu super league.

Timu ya MTV Maxi Bullets, ya chigawo chakumwera, idatuluka pamene mkulu komanso mwini wa timuyi Maxwell Kapanda adalengeza kuti timu yake yasiya kusewera masewera ake otsala mu league yaikulu ya m’dziko muno kamba koti akuluakulu omwe amayendetsa league yaikulu kuno Ku Malawi amakondera ma timu ena.

Izi zidali chomwechi pamene bungwe la Super League of Malawi (SULOM) idalengeza kuti timu ya Max Bullets idaluza mapointi atatu itakana kupitiliza masewero awo omwe adali 1 kwa 1 ndi timu ya Epac potsatira kukondera komwe amachita oimbira masewera amenewa.

Pakadali pano, timu yochokera m’chigawo chapakati ya master security yalowa mu league yaikulu ya m’dziko muno ndipo pano tikudikilira matimu ena awiri kuchokera chigawo chakumpoto komaso chigawo chakummwera kuti amalize malo awiri omwe atsala kuti matimu omwe atamenye chaka cha mawa akwane 16.

Advertisement

12 Comments

  1. TAPHUNZIRAPO CHANI MATIMU, MUYENELA KUMALIMBIKIRA KUYAMBA PACHIYAMBI OSADIKIRA KUTI TIKAMAZAKUMANA NDI TEAM YAKUTI TIZATOLERA MA POINTS, CIVO YANGA INE!!! BOLA USAKHALE ULENDO WAMPAKANAMPAKANA.

Comments are closed.