A polisi akusakabe yemwe adapha mlaliki Wame

Advertisement
shadrek-wame

A polisi m’boma la Salima ati akusakabe yemwe adapha mlaliki odziwika bwino mdziko muno a Shadrek Wame.

Oyankhulira a polisi m’bomali a Gift Chitowe ndiomwe anena izi dzulo lolemba pa 31 Okutobala.

shadrek-wame
A Wame adachita kuphedwa.

A Chitowe ati iwo anakhazikitsa kafukufuku ofuna kugwira yemwe adachita chipongwe chimenechi ndipo anaonjezera kuti pakadali pano kafukufukuyu adakali mkati.

Mneneli wa a polisiyu anatsutsa mwantu wagalu mphekesera zomwe zikuveka zoti iwowo agwira yemwe akuganizilidwa kut anapanga chipongwechi.

Iwo ana izi sizoona ndipo anakanaso mphekesera ina yomweso yaveka kuti munthu oganizilidwayo anaphedwa ndi anthu olusa mdelaro. A Chitowe ati zosezi ndizabodza.

“Ife a polisi tikufuna titsutse mphekesera imeneyo chifukwa palibe yemwe wabwera ndikutitsimikizira kuti yemwe adapha malemu a Wame wamangidwa kapena waphedwa ndi anthu olusa, choncho zosezo ndizabodza. Chomwe tikudziwa ife ndichakuti kafukufuku ofuna kugwira yemwe adachita chipongwe chimenechi adakali mkati.”

Atelo a Chitowe. Iwo aonjezera kunena kuti anthu osiyanasiyana akuwatsina khutu momwe angampezere nkulu yemwe adachita chipongwe chimenechi.

Mlaliki Wame adapezeka ataphedwa mnyumba mwake mmawa wa la chisanu pa 28 Okutobala.

Ma lipoti akuonetsa kuti malemuwa adaphedwa ndi wantchito wawo yemwe adasemphana naye chichewa pankhani ya chimanga. Malemu a Shadreck Wame adabadwa mchaka cha 1940.

Iwo ankachokera mmudzi wa Mwanzalamba, mdera la mfumu ya ikulu Kambalame m’boma lomwelo la Salima ndipo aikidwa mmanda dzulo lolemba pa Okutobala 31.