A polisi akusakabe yemwe adapha mlaliki Wame


shadrek-wame

A polisi m’boma la Salima ati akusakabe yemwe adapha mlaliki odziwika bwino mdziko muno a Shadrek Wame.

Oyankhulira a polisi m’bomali a Gift Chitowe ndiomwe anena izi dzulo lolemba pa 31 Okutobala.

shadrek-wame
A Wame adachita kuphedwa.

A Chitowe ati iwo anakhazikitsa kafukufuku ofuna kugwira yemwe adachita chipongwe chimenechi ndipo anaonjezera kuti pakadali pano kafukufukuyu adakali mkati.

Mneneli wa a polisiyu anatsutsa mwantu wagalu mphekesera zomwe zikuveka zoti iwowo agwira yemwe akuganizilidwa kut anapanga chipongwechi.

Iwo ana izi sizoona ndipo anakanaso mphekesera ina yomweso yaveka kuti munthu oganizilidwayo anaphedwa ndi anthu olusa mdelaro. A Chitowe ati zosezi ndizabodza.

“Ife a polisi tikufuna titsutse mphekesera imeneyo chifukwa palibe yemwe wabwera ndikutitsimikizira kuti yemwe adapha malemu a Wame wamangidwa kapena waphedwa ndi anthu olusa, choncho zosezo ndizabodza. Chomwe tikudziwa ife ndichakuti kafukufuku ofuna kugwira yemwe adachita chipongwe chimenechi adakali mkati.”

Atelo a Chitowe. Iwo aonjezera kunena kuti anthu osiyanasiyana akuwatsina khutu momwe angampezere nkulu yemwe adachita chipongwe chimenechi.

Mlaliki Wame adapezeka ataphedwa mnyumba mwake mmawa wa la chisanu pa 28 Okutobala.

Ma lipoti akuonetsa kuti malemuwa adaphedwa ndi wantchito wawo yemwe adasemphana naye chichewa pankhani ya chimanga. Malemu a Shadreck Wame adabadwa mchaka cha 1940.

Iwo ankachokera mmudzi wa Mwanzalamba, mdera la mfumu ya ikulu Kambalame m’boma lomwelo la Salima ndipo aikidwa mmanda dzulo lolemba pa Okutobala 31.

67 thoughts on “A polisi akusakabe yemwe adapha mlaliki Wame

  1. Akanapezeka mwa changu mukanati anthu akuthandizeni kupeza koma osati kukuthandizani kugwila munthuyo koma kumu otchaso ndemukana va zoti bwelani muzatenge phulusa kuno

  2. Delta Hotels Toronto,is Currently recruiting able bodied workers from all over the world to fill in the following vacant positions such as:Room Services, Hotel Receptionists, Kitchen References,Hotel drivers, Pool Management, Gardeners, Security Services etc….Application lasts from now till 30th November 2016….for Applicants in America/Europe/ Asia kindly whatsapp miss Lisa on +16474920576 and for our African applicants whatsapp mr Josh on +221708781126 for guidance. …Wish you all the best of luck and will be delighted to meet you all here soon….Thanks….

  3. Aja anaba ndala pa petroda Ku Lilongwe anagwida what more uyu mwazi wa munthu otsalakwa ukumutsaka.popano apedzeke satana amenei.

  4. Mhuu!! Mpaka kupha munthu wa Mulungu?? Ayitu Ambuye chitanayeni munthu ameneyu ndikumuzindikirisa kuti palibe chobisika pansi pathambo,

  5. by this way am sure simungampedze cz nayenso ali pomwepa kuwerenga ndi kuona ma post oterewa. mukumpanga encourage kukhala munthu ochenjera and kut athawire kutali. zinafunika kachetechete ife mudzangotiudza kut munthuyo/ anthuwo agwidwa. that’s all.

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading