Samalani ziwalo zanu zobisika, odula ziwalo ayambilanso

Advertisement
knife-blood

Palibe kothawila mu dziko muno. Pa nthawi imene chuma chasokonekela, chiopsezo cha njala chakulira ndipo anthu ena oipa akuchita nkhanza anthu a chi alubino, kwabwelanso anthu odula ziwalo.

Mnyamata wina wa zaka 18 ali pa ululu osaneneka pa chipatala chachikulu cha Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe, anthu a chiwembu atamudula ziwalo zake zobisika. Izi zinachitika mu boma la Nkhoktakota.

Malingana ndi mkulu wa apolisi pa polisi ya Nkhunga ya mu boma la Nkhotakota, a Labani Makalani, chiwembu chomudula maliseche mkuluyi chinachitika lachiwiri pa esiteti ya Illovo ya mu bomalo.

knife-bloodA Makalani anauza ife kuti zigawengazo zimafuna kukagulitsa maliseche a munthuyo.

Malawi24 yauzidwanso kuti mmodzi mwa zigawengazo wagwidwa ndipo ali mmanja mwa a Polisi pamene anzake ane akufunidwa ndi a Polisi.

A Makalani ananenanso kuti mnyamata amene anadulidwa malisecheyu ndi mkulu ochita malonda a Kabaza. Iye anapezedwa ndi a Polisi ali mu ululu osaneneka zigawengazo zitamusiya kuti afe.

Kupatulapo kuti anamudula ziwalo zake zobisika, mnyamatayu anapezeka ndi bala mmutu komanso anamuthyola msagwada.

Mkulu wa zaka 41, a Rangerson Mashikudu, ndi amene amangidwa ndi apolisi okhudzana ndi chiwembu chimenechi.

Zomvetsa chisoni kwambiri ndi zokuti ngakhalae apolisi anapeza ziwalo zimene zinadulidwazi, achipatala ati sangakwanitse kuzibwezeletsaponso pa munthuyu.