Mzika za dziko lino zapitiliza kulira kuti malamulo amene amagwilitsidwa ntchito pomanga ndi kumenya anthu opezeka akuyenda usiku athe.
Anthu akupempha kuti malamulo amenewa asinthidwe Kamba koti malamulowa amangopweteka anthu osauka. Mwa zina, malamulowa amapatsa mphamvu apolisi kuti anjate ndi kuimba mulandu anthu omwe apezeka akuyenda usiku.
Ophunzira wina wa ku Yunivesite amene sanafune kutchulidwa dzina koma wamangidwapo pachifukwa choyenda usiku anauza mtolankhani wathu kuti lamulo limene limatchuka kuti la vakabu limangopweteka amphawi kusiya olemera amene ali ndi kuthekela kopalamula milandu yoopsa usiku.
“Ine tsiku lina ndimachokela ku layibulale ndi amzanga. Kumene timagona ndi patali ndi sukulu. Ndiye tikupita kogona tinakumana ndi apolisi amene anayamba kutichita nkhanza ati chifukwa timayenda usiku. Pamapeto anatimanga ndi kutitsekela mu chitokosi,” anadandaula motero ophunzilayo.
Mkulu wa bungwe lomwe limaphunzitsa, kulangiza ndi kuthandiza anthu pa nkhani za ufulu wawo la CHREAA a Victor Mhango anauza atolankhani a MANA kuti nthawi yakwana kuti dziko lino lithetse malamulo omanga anthu opezeka akuyenda usiku.
“Bungwe lathu ndiye likulimbana ndi makhalidwe omanga anthu opezeka akuyenda usiku, posachedwapa tinakumana ndi atolankhani amene tinawaphunzitsa kalembedwe ka nkhani zokhudza vakabu. Tinawauza azifotokoza kuti ndi nkhanza kumanga anthu pa chifukwa choyenda usiku,” anatero a Mhango.
A Mhango ananenanso kuti bungwe lawo likukumana ndi apolisi ndi oweluza milandu kuwalimbikitsa kuti aleke kulanga anthu opezeka akuyenda usiku.
Mneneri wa ku mabwalo a milandu, a bamboo Mlenga Mvula ananena kuti milandu ya anthu omangidwa Kamba kopezeka akuyenda usiku ikuchulukila.
“Nthawi zambiri ife a mabwalo basi timangowapatsa chilango choti alipire chindapusa, sitingawatumize kundende chifukwa ndiye kungadzadze,” anatero a Mvula.
Kugwira oyenda usiku sikolakwika koma pazikhala,malo ake,nthawi yake,
Osati pabara akumwa
akagwire zigawenga
mukulira chan? Ine ndimachoka kuntchito usiku sanayambe andigwirapo, nanga inu mmakhala mukuchoka kuti? Isathe vakabu ndichitetezo chathu cha anthu olungama ife. Mukufuna muzitimenya ngati kale eti? Nkumatilanda zinthu
Inde mbava zikudan nd vacab
mbava ndi zimene zikufuna kuti vakabu ithe aziba bwino
Kulephera kugwira mbava zenizeni kumakagwira osalakwa futseki police
Apolice ndi amene amabaso kwambili mbava
Zoona zimenezo, malamulo asinthidwe chifukwa a polisi a Malawi alibe luso pantchito yawo. Amangofikira kumenya ndipo nthawi zina amamenya anthu osalakwa ndipo amadziwa mochedwa kuti amenya munthu wosalakwa. Mu Johannesburg mtawuni a polisi akapeza munthu akuyenda usiku choyamba amamusecha kuti awone ngati ali ndi zida ngati mpeni kapena mfuti, kenako amamfunsa kumene akupita, pomalizira pake amamfunsa identification document. Ngati zonse zilibwino amamutaya. Nanga zikuvuta bwanji Malawi dziko la mtendere?
Ndiye Bwino Tizimwa Mpaka Kucha Mbeeee
Malawi slowly changing into Mozambique,ndi ukayidi umenewo
Mapazi awo azilonda komaso akapolo achabechabe lamulo lichoke ndilabwino koma ma enforcers sadziwa ntchito komaso yanthauzo lake salidziwa amangopanga zinthu muchimbulimbuli so the best way is to elliminate the law completely.thank u.
Izi Ndiye zamveka bwino bwanji, muzingolemba mu chichewa basi
Ine ndye ndilibe nawo mau pandalama zomwe anditengela n amachita kumandidikila malo amodzi omwe omwe koma chosecho akuziwa kuti ndimapanga biznes yoweluka mazulo
Malamulowo pawokha ndi abwinobwino koma the way our police officers are utilizing them eish zovuta kumvesa, i remember ndinagwidwa vakabu 11pm galimoto yanga ili pambalipo, kundimenya , ndikundibera ndalama zanga zonse, mmodzi kukwera nane mgalimoto mwanga ulendo waku cell, spent a night mu cell. Have heard alot of similar stories. Enforcement ya lamuloli ndi yomwe ifuna kusinthidwa
Ndinagwidwapo ineo ku Kanjedza Lodge yet ndinali ndi Id,Driving Licence,psssport,and nthawi imeneyo ndimachindana mchibwezi changa,atatigwira anapita nafe pa Limbe police station,usikuo ku station kwaoko wapolice wina anandichindaso mondiumilidza
apolice akumalawi sanayendepo mayiko ena m’chifukwa chake akadali m’tulo.masana timafuna ndalama ya ndiwo usiku ya ufa.
vakabu ndi umbava wa apolisi
Instead of kumamka nayendera makomo kut azigwira mbava zavutazi koma kuyenda ma bar kumafuna ati ndalama zaulesi akamawatulusa anthuwo
these laws do not reflect the reality on glound.. imagn uli pa night shift & or overtime & u want to go home early kenako ukumane ndi vakabu.. its high time we change thsese laws otherwise akupanga benefit ndi a police…
Mukuthandawuza kuti achose moti anthu azi ngoyenda chisawawa usiku onse?kaya wolezera,akuba, afiti otamba,mahule, ma vendor etc
Eti mpaka disturbing business men in rest houses. Akakupeza ukuyenda usiku pa msewu akumenye, akupeze ukugona ku rest house akumangenso. It once happened to me in 2011. I had all the legal documents but was nothing to them, POLICIA CORRUPTOS E ESTÚPIDOS!
Ine ihate this law coz imakondera, munthu akakhala pa galimoto samamugwira kma woyenda pansi nde kumugwira, nde zichan zimenezo. Ndekut lamuloli nd la anthu osauka bas? Aganizepo bwino pamenepo.
Zoona chifikwa a police a ena udindo wawo kapena ntchito yawo saitenga munthu ampeza sakuthawa koma amayamba kumumenya komanso munthu oti wagwidwa vakabu mumveee bail yokhayo ngati kuti anaba zisithe kapena malamulo achepe mphamvu
Apolice avcb ndiwomwe akumaba kwambili ndipo apolice sakuyenela kwaletsa anthu kuyenda usiku ? Koma akawapenza awafunse chifukwa chomwe akuyendela usikuo
Dat true zanyanya ena amakhala akuchokera kuntchito,kumaliro,mapephero ndi malo osiyana siyana kma apolice alibe nazo amangoti mukanenera konko akudziwa kuti mulandu wa vakabu munthu sukana chimakhala chili chani..?
KUGADA USIKU KUSATHE BCOZ MBAVA ZIMACHITA MANTHA KUYENDA! KOMA AVAKABUWO SAKUGWIRITSA NTCHITO BWINO UDINDO WAWO.
tink deeply my fell malawians..akachotsa lamulo ili..one day tizakhalanxo tikulira..coz most people that walk during nyt..amakhala a upandu
Savages in comoufrages
Anthu ena amagwila ntchito usiku nde kukumanga opanda reason yomveka bwino a polisi tiziwalodza. Aziyenda usiku for protection yes osati kukapanga ndalama zomwela mowa ndima hule.
Lamuloli ndilabwino koma vuto apolice anapezerapo pothesera mavuto akunyumba kwawo.They missuse power ena amati vakabu akuba ndi iwowo FOR example am late ndikuyenda usiku coz ndikuchoka kuxovuta ukawafoktokozera chabwino kuwapempha kandisiyeni kwathu use ur car for u to blieve am not thief amakana moreova galimoto fuel akugwirisa ntchitozo Ndizatonxe our taxe
Ulemu ndiofunika apolice ku rest house anthu amagona maliseche inu mumagogoda ngati munthu waba apolice ambiri ndiakuba, ndiomwenso amasokoneza kwambiri munt.hu osamufunsabwinobwino ai mwayambakummenya samalani ndichifukwa apolice ambiri timaphedwa chifukwa cha moyooipa pewani moyoochitila nkhaza dzanufe
This is 2016 people do business even at night ..even having fun at night is not a crime …wake up
Kungoti sionse oyenda usiku ali akuba ena amakhala adeledwa , ena amaperekeza matenda kuchipatala mwina maliro amene koma azingofufuza bwino bwino mwina nkumaqapelekeza npaka kwao
Timasongoneza zinthu, kuyenda usiku sikuti ndiwe wachiwembu kapenna okuba ayi, kungoti Amalawi kuyipa ntima kunachuluka
Why arresting in rest houses?
Amatibela amenewa apolisiwa pafunika zitheletu Zimenezi apeze zochita zina amapezeka akumutenga munthu kumalo ogona alendo atagona akut tidziwane mapeto make unva tiye kwera galmoto ukanenela konko ndichilungamo kutelo
Amene akumamangawo akayese kumanga kumangochi…azasiyaaaa
zithe zavakabu mwinatingawoneko mwezi kugona six okolock zoon olomwezi waladan osawuna zoona
?
Sizolakwika koma pakufunika aziyamba chamma 9 koloko
Asalichoseyi umbava uzachuluka ,muzayamba kudandaula so kuti bomali they are not protecting the citizens yet mkufuna alichose, komaso what is latest time kuti everyone should be indoors? ????
Ngati dziko likulowa pansi vuto si oyenda usiku …….cashgate bwa!?
I hate police, vacub n neibrhood. fuck dem all. anthu amene akubwenzeresa dziko lino mbuyo.
Kkkkkk
Palimbe kusintha malamulo apa malamulo awa ndi a kale kale take it easy the law will 4you the one who take night to be your thoughts going
Kwa inu nonse amene mukufuna kuti vakabu ithe mukufuna kuti muziba? Kapene mukufuna chan? Zimenenzo zisachitike vakabu ipitilile kugwila ntchito yotamandikai umbamva uthe
This law is just there to make this country poor how can the all people go to bed @ 6 in the evening and start working @ 8 in the morning and expect to be economically sound, Malawi wake up.police must work around the clock and in truth there are more criminal activities happening during the day than at night in this country.laziness laziness until when???wake up.
Kkkkkkk wandiwaza heavy. Timagwira ntchito ma hrs ochepa,,,omweo timapeza nthawi yopangira bawo while at work.
Ayi lithe lamuloli coz akutibera heavy….this system is nt our frend.
ये सांस भी मेरी, मेरी ना रही,
ऐ इश्क जबसे तू है हमारी…
दोनों हम है तलाश मे चैन के,
खो गया हैं जो साथ मेरे यार के These are my breath, I’m not,
AI love you, since our …
We are both in search of peace,
Who lost my love
Rougue and Vagabond is one of the out dated laws which needs to be reviewed
Best news l heard in years, while other countries are trying to have 24hr cities to make alot of revenew for their economies ife kuno tikadalimbana ndi malamulo a chisamunda ngati vacab work up malawi, dzuka malawi dzuka, those police persons are suppose to protect drankers not aresting them.
Sionse oyenda utsiku ali akuba mwamvaaaaaaa
Ndiuchisiru kumene kumenya munthu woyenda usiku ndikumanga .bwanji bola likulephela uyu akumalimbikitsa nchitidwe wokupha Albino.Absolute no xance.
Asamangwire
Ndeye kuti dziko lanthu laphwanyanso lamuro lofunikira kobosi, enanu mukufuna mzakaba mosavuta
Ayi zisathe chifukwa umbanda ndi kumba kukula and dziko lili lonse limatelo koma amalawi ufulu meautengela pamgong,o ufulu uli ndi malore ake mawa ndi inu iwe ukupangidwa chiwembu uzifzalira kuti Boma sili kuchitapo kathu dzikotu tikuliwononva tokha chifukwa ati ufulu
Lisathe ia zaumbava basi kkkkkkkk no yending during naiti kkkkk
ndebwino tmasmowa kut tkamwera kut koz tym ife imapezeka nyt ka….winawe eish ilopatu apa asaaa!!!!!
6:00 amatikwapula twn IJA inali usiku
Kuba kwachuluka mmalo motetezedwa tinayamba kuiiopa police ngakhale masana omwe
Ine ndilibe nayo mau Police ndinagwidwa ndikuchokela ku ntchito koma makofi ndinalandilao ngati ndatukwana boma kenako amvekere zipulumuse wekha
Khani koma imeneyo
Chifukwa Amalawi Akufuna Kt Awabele Obwela Onse Chuma Chikhale Chatu, Malawi Oyeeeee!!!!!
Zithe Amanyanya Agalu Amenewa !Kodi Sakumalandila
Kkkkkkkk,no comment Malawi sazatheka zomanga anthu oyenda utsiku dzithe kk,Malawi zuka plz
Mbava zikubisala mmabottle store.
Koma oaanama a police akuonjeza nthawi zina akugwila anthu osalakwa ndikumawa menya zingachite bwino zitatha bas
Kusintha yayi
Mbankhunkhu awo wankhumba visinthe
Zithe basi tizimwa mofatsa bawa no cheu cheu
Vakabu ndi utsamunda basi
Umphawi umawapweteka apolicewa kwambiri thats why amapanga zosiyana ndizomwe lamuloli likunena, ngat lamulo likuti munthu akuyenela kumangidwa akapezeka pa public place akuoneka kuti alibe chochita, so apolicewa akumatimanga akatipeza ku resthouse so my question to them is,,,kod resthouse ndi public place??? Nanga ngat ili public place timalipila chifukwa chan??? Fuck_them_all, i stand on truth #osaopa…
why not azimangidwa.
Amakayendela uvakabu mu ma botolo storo
Cholinga mudziba momasuka,
Kkkkkkk koma kwathu ku malawi,,,,, tsopano ndalama mkumachita thawi yanji? Ndiekuti kulibe tchito zina za overtime? Athu akuenera kuenda 24hrs apolice nawoso 24hrs akamudabwa muthu kumufusa wachilungamo sasowa. Koma zoti basi kungokumana ndi police kuthawa ndie Juberg depotee imeneyo.
Ine ndili kumbali yaboma oyenda usiku ochokela kumowa ndiosowa kochokela amangidwe
Umphawi umawapweteka apolicewa kwambiri thats why amapanga zosiyana ndizomwe lamuloli likunena, ngat lamulo likuti munthu akuyenela kumangidwa akapezeka pa public place akuoneka kuti alibe chochita, so apolicewa akumatimanga akatipeza ku resthouse so my question to them is,,,kod resthouse ndi public place??? Nanga ngat ili public place timalipila chifukwa chan??? Fuck_them_all, i stand on truth #osaopa…
Umphawi umawapweteka apolicewa kwambiri thats why amapanga zosiyana ndizomwe lamuloli likunena, ngat lamulo likuti munthu akuyenela kumangidwa akapezeka pa public place akuoneka kuti alibe chochita, so apolicewa akumatimanga akatipeza ku resthouse so my question to them is,,,kod resthouse ndi public place??? Nanga ngat ili public place timalipila chifukwa chan??? Fuck_them_all, i stand on truth #osaopa…
Umphawi umawapweteka apolicewa kwambiri thats why amapanga zosiyana ndizomwe lamuloli likunena, ngat lamulo likuti munthu akuyenela kumangidwa akapezeka pa public place akuoneka kuti alibe chochita, so apolicewa akumatimanga akatipeza ku resthouse so my question to them is,,,kod resthouse ndi public place??? Nanga ngat ili public place timalipila chifukwa chan??? Fuck_them_all, i stand on truth #osaopa…
Mbava zikufuna ufulu wao kkkkkk
12 koloko yawutsiku ukuendaenda ufuna chani amangidwe basi.
Pachithuzipo uyo watenga nkhwangwayo samukhapa nayo mzakeyo kma?
Lamuloli lilibwino hevy,koma vuto ndi apolice
oyenda utsiku chisawawa atengedwe basi,and mzimenyedwa. Police plz go ahead
mukufuna mupezelepo mwayi muziba eeti. timanga aliyese wopezeka akuyenda usiku basi.
Deall,, Azigwidwa Oyenda Usikuwo Ndi Zoonadi. Koma Nanga Masana, Popedzanso Amatigwira Mu Limbe-mu, Ndi Usana Omwe Tisamayende?
Kkkk Komaditu Kwinikweni ukavala ngati ukuchokera kuchigayo ndie shaaa zavuta kodi mmesa tili ndi ufulu wakavalidwenso?
“Pamenepo! Dziko Lathu, Koma Zoona Tidziyenda Ngati Tili Mziko La Eniwake? Tili Ndi Ufulu Oyenda Masana, Ufulu Wa Mavalidwe.
cholinga aziba? palibe zimenezo asasinthe
Our police its ful of sheat they thnk onse oyenda usiku ndi akuba
Vakabu yoyamba 6:30 koma police yafikapo amwene.
Zimanyansa kwambiri za vakabo mpaka kukalowa mma Rest house kumanga anthu opanda zifukwa, athee!!!!
Ine atandiwuza kuti ndisankhe pakati pa Apolisi ndi a G4s ndikhoza kusankha a G4s.
Namchichiyi akadzamwalura tidzaupeza mtendere
Poti utayambe ndiwe
Ine zokufazo iwalani man
Lisathe angatiphe.
ine ndimakhaulitsa vakabu usiku ndimavula zovala kunyamula mujumbo ndimayenda maliseche ena akhala akuthawapo a vakabu kuyesa mfiti …
zimenezo ndezacamba mukufuna muztbela bwno?
Vuto apolice anapezera pobera anthu, vacab siyolakwika koma akumayamba 8koloko mmala mwa 10koloko
Choyamba ndikuthokoza chifukwa cholemba nkhani mu CHICHEWA pali nkhani zina komanso zambili zomwe zimafunika kuti a Malawi azizimva bwino ngati m’mene amachitila mayiko azathu.
KUMANGA ANTHU USIKU PAZIFUKWA ZODZIWA OKHA KUSATHE
– Izitu zimachitika mayiko ambili munthu amene afuna asamangigwe ndibwino aziyenda ndi mapepala omuloleza kuyenda usiku
– Izitu zikhoza kuchepetsa umbamva umene wachuluka dziko lathu la Nyasaland.
Anzanu amadyera momwemo
Anthu amene akuti zithewo nde mbava zikulu zikulu ziku funa zikaba zizi enda mofewa kazi gwilani usiku imakhala nthawi yogona amapita kuti bola akanati adzimufufuza munthu bwino bwino asana mugwile ndipoveka nanga munthu uzienda usiku 3 koloko sugwila ntchito umatani kazizi umbudzani mbavazi usikuwu isathe dihlu yo mbuzi imadya pamene ai mangilila akugwilani muku choka kwakuba muku enela ku gawana kumene adziku siyani ndi ngini zoti mwaomba kwina nde sali ntown tu apolice wo tu
sunakumane nawoko a bvakabu iwe,anthu amenewa amazuza,olo akupeze ndi makiyi agalimoto savomera kukusiya mpakana galimoto kugona pamene unayimikapo,udzaziwona ukadzakumana nawo.coz siwonse amene amayenda usiku ncholinga chokaba.
Zoti anzanu akuphedwa usiku wu mumazi dziwa apolice saku siya ku mene iwe una ku manako ndiwa kuba panjila ndikungo ku secha osaku peza ndikanthu ndikuku uza kuti ulibe dohla kazi vaya mesa amaku siyila mnpeni kuti uzikumbukila kuenda ndi dohla usiku zotiso akuba ama panga hayala magalimoto omwewa simudziwa ama funa aku welenge chifukwa amakhala kuti adziwa kuti suli wekha amzako ajowa mnpanda wawina akukapanga atuck kumeneko
mwanena zoonadi man akufuna aziba mwaufulu kkkkkkkkkk amangidwe basi woyenda usiku.
Kkkkk eti man anthu aku bakila zoti zithe chifukwa sana kumaneko nda galu amichombo usiku ndinkani akungo yankhula kale ukamaenda usiku chomwe umaopa chinali fisi mankwala ake tima enda ndi tochi paja fisi amathawa akango ona kuwala kwa tochi pano nditokha tokha tiziopana nkhani yake kwagwa n.dima kkkk
pano vakabu ndimasana omwe anthu akumangidwa and pano akhotinso akweza chindapusa kufika pa k7000.
Nnachita kumva wapolisi akulankhulana ndi judge wina wake pa chichiri ku high court akuti, maluzi ndiye apweteka bwanji, winayo amvekere, osakangogwira vakabu usiku uno bwanji azidzanyema pang’ono pang’ono kuti tiwataye basi mawa siukhalanso mmaluzi. It’s a system and sad that dzikoli is just rotten from top to toe
Yes zikumachitadi bro.koma ichi sichifukwa chokwanira kuti vakabu isiye kugwira ntchito yake.tangoganizani bro umbava ndi uchigandanga ukuchitika pamene vakabuyo ikugwira tchito yake what more ngati kulibe vakabu zingakhale zotani?
Vakabu yili ndi ubwino wambiri kwabasi. Isaphatikizidwe ndi nkhani ya corruption,aMalawi wasangosanduka mnkhalidwe wanthu ndipo tili pa mmbalambanda dziko lonse la pansi.
The law is good braz, but the intentions of police in handling the matter makes it look bad. Tiyeni zinthu zina tizidziongola mosalekelera zikamakhota. Those in authority take advantage of our ignorance and disunity
Karma is waiting thats why azifa mosaziwika bwino ,,
a judge on rogue and vagabond ? Lier .these are dealt in magistrate court .leave judges alone .
Yes it was a certain her worship waku magistrate. The magistrate word did just run away from me. Take off the liar word, mmakonza basi mwinanso ndinu akonko mukuzidziwa bwino kuti tikudziwa izo mmachita
kod thom wanenako kut vacab ithe?mungoyankha musanamunvetsetse bwa?hs just Saying what he heard.
Masana mumakhala kuti kkkk
lamulo linali labwino koma apolice, anapezelapo mwayi wobela ndalama za amphawi, bcoz 8koloko ayamba kale kugwila anthu ati vakabu, nde , komanso lamuloli kuti lithe kukhala umbava wazaoneni utsiku, nde tingoti lithe chifukwa apolice wa agugwila nthawi yabwino komanso sakumamvesa ukamawadandaulila kumene ukupita kapena komwe wachoka akungoti vakabu basi…
lichoke
Sionse omwe amaenda usiku amakhala ndi zolinga zenizeni,ambiri amakhala akuba, Ubwino wake mukamaberedwa ovutika ndinu nomwe.
Lamulo loipa ili amakumanga even kukupeza ku resthouse ukupepesa usiku akut mpaka awone marriage certificate
lithediii ndizikanika kumwera zanga kamba koti vacabuuu aaaaaa,
chodabwisa okuba samagwila amagwila olezela okhaokha kk
ndikugwilizana nazo zimenezo makamaka enafe timagwira ntchino ya u balaman,,amachita kunditchera ndikaweruka cha m’ma 2 kuti andikolopore timachange muzina la Vakabu,,Futsek vakabu!!!
Isathe imasangalatsa akabwera tikamathawa timaphunzira kuzemba
Lamulo limeneli lithed amatmanga osalakwa pamene bava zikuba ndalama k capital hill osawagwila
Lamuloli ndi labwino. Only that a police akulipanga abuse. Nawonso alowa kubera anthu using lamulo lomweli. Just like Paul Banda’s song. “Ambiri tikulephera kugwiritsa…… Ndipo zimaoneka ngati zoipa
Uchitsilu basi mukufuna mudzitibela ndikutigwiririla azinkazi athu iya
Nanga wa pa galimoto?
Apagalimoto naonso asamaende usiku
Vakabu Isathe Kma Akhale Nd Nthaw Yoyambira Yeniyeni Osati 6 O’clock, Ambiri Amakhala Aderedwa Ku Ntchito nd kuma Business Amamangidwa Osalakwa
Kupusa….mtima okuba basi
Anthu azilephera kudya ndalama zawo usiku chifukwa cha mbuzi za a police demet
palibeeee…litha bwanj..? lisathe kulibwino ndizikumana ndiwavakabu than mdula ziwalo..
M’dani wa lamulo ndi muthu amene amaphwanya lamulo.
Apolice amaonjeza. Vakabu yasanduka fundraising activity.
Kkkkkkkk
wakula ndi umava bac
Kut aziba opanda nkhawa et!
nkhani zake?mutiuze kaye zifukwa zomveka zomwe mukufuna kuthesera lamulo limeneli,,umbava eti?
cholinga muziba bwino?
Mbabva
Malawi is indeed the world’s poorest country.
Chimenechi nkukhala chifukwa chomangira munthu
Koma ufulu pamenepadi ukuphwanyidwa. Bwanji osalimbana ndiumbava koma? Oyenda pagalimoto kaya akukaba osamumanga koma ochoka kumowa akupita kunyumba kwake kulimbana naye.