20 August 2016 Last updated at: 7:41 AM

Oyenda usiku asamamangidwe; a Malawi akufuna malamulo a vakabu asinthidwe

Mzika za dziko lino zapitiliza kulira kuti malamulo amene amagwilitsidwa ntchito pomanga ndi kumenya anthu opezeka akuyenda usiku athe.

police malawi

A polisi akumanga anthu zedi.

Anthu akupempha kuti malamulo amenewa asinthidwe Kamba koti malamulowa amangopweteka anthu osauka. Mwa zina, malamulowa amapatsa mphamvu apolisi kuti anjate ndi kuimba mulandu anthu omwe apezeka akuyenda usiku.

Ophunzira wina wa ku Yunivesite amene sanafune kutchulidwa dzina koma wamangidwapo pachifukwa choyenda usiku anauza mtolankhani wathu kuti lamulo limene limatchuka kuti la vakabu limangopweteka amphawi kusiya olemera amene ali ndi kuthekela kopalamula milandu yoopsa usiku.

“Ine tsiku lina ndimachokela ku layibulale ndi amzanga. Kumene timagona ndi patali ndi sukulu. Ndiye tikupita kogona tinakumana ndi apolisi amene anayamba kutichita nkhanza ati chifukwa timayenda usiku. Pamapeto anatimanga ndi kutitsekela mu chitokosi,” anadandaula motero ophunzilayo.

Mkulu wa bungwe lomwe limaphunzitsa, kulangiza ndi kuthandiza anthu pa nkhani za ufulu wawo la CHREAA a Victor Mhango anauza atolankhani a MANA kuti nthawi yakwana kuti dziko lino lithetse malamulo omanga anthu opezeka akuyenda usiku.

Victor Mhango

Mhango; Malamula a vakabu aunikiredwenso.

“Bungwe lathu ndiye likulimbana ndi makhalidwe omanga anthu opezeka akuyenda usiku, posachedwapa tinakumana ndi atolankhani amene tinawaphunzitsa kalembedwe ka nkhani zokhudza vakabu. Tinawauza azifotokoza kuti ndi nkhanza kumanga anthu pa chifukwa choyenda usiku,” anatero a Mhango.

A Mhango ananenanso kuti bungwe lawo likukumana ndi apolisi ndi oweluza milandu kuwalimbikitsa kuti aleke kulanga anthu opezeka akuyenda usiku.

Mneneri wa ku mabwalo a milandu, a bamboo Mlenga Mvula ananena kuti milandu ya anthu omangidwa Kamba kopezeka akuyenda usiku ikuchulukila.

“Nthawi zambiri ife a mabwalo basi timangowapatsa chilango choti alipire chindapusa, sitingawatumize kundende chifukwa ndiye kungadzadze,” anatero a Mvula.144 Comments On "Oyenda usiku asamamangidwe; a Malawi akufuna malamulo a vakabu asinthidwe"