Madzi asefukira ku mpoto- watelo Unduna wa za Madzi

Advertisement

Unduna wa za Madzi ndi Ukhondo m’dziko muno wati kukhala madzi asefukira mu mitsinje yambiri ya m’chigawo cha kumpoto kwa dziko lino kuphatikiza ma dera amene ali m’mbali mwa nyanja kwa sabata yathunthu kuyambira pa 12 mpaka pa 18 April chaka chino.

Undunawu wati kusefukira kwa madziku kudza chifukwa cha mvula yochuluka yomwe ikugwa m’madera a ku mpoto yomwe ili ndi kuthekera kokhutitsa mitsinje zomwe zizetse kusefukira.

Mu kalata yake ya undunawu yawonetsa kuti mitsinje yomwe ikhonza kusefuka ndi monga North Rukuru, South Rukuru, Hara, Nyungwe, Wovwe, Songwe, Kyungu, Lufilya, Limphasa, Nkhula , Lipimbi ,Dwambazi, Dwangwa, Bua,Luweyo , Kajilirw, Kakwewa, Kalungulu, Kalwe, Luchelemu , Linthipe, Lingadzi, Lifidzi ndi Nadzipulu.

Undunawu wachenjeza anthu okhala moyandikira mitsinjeyi kuti akhale tcheru komanso kusuntha m’madela a chiopsezowa ndi kukakhala malo otetezeka omwe anakhazikitsidwa kuopa kutaya miyoyo chifukwa cha kusefukira kwa madziku.

Pakadali pano, madzi akusefukira mwa kachetechete kamba ka kukwera kwa madzi mu nyanja ya Malawi kukupitilira kusautsa anthu ndi ma business awo maka amene akukhala m’mbali mwa nyanjayi m’maboma monga Nkhatabay, Mangochi, Salima, Nkhotakota mwa ena.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.