Mpingo wa Katolika mu Diocese ya Zomba watulutsa chikalata choonetsa kukhumudwa ndi wansembe wawo a Thomas Muhosha amene anamangidwa poganizilidwa kuti anatengapo mbali pa imfa ya a Macdonald Masambuka.
Malinga ndi chikalatachi, a Muhosha aimitsidwa tsopano ngati wansembe. Chikalatachi chanenanso kuti Mpingo wa Katolika umalemekeza moyo wa munthu aliyense ndipo supeleka mphamvu yochotsa moyo.
A Muhosha anjatidwa pamene Apolisi akufufuza anthu amene anapha a Masambuka amene anali munthu wa chi albino.
Imfa ya a Masambuka ndi kafukufuku amene watsatila zaonetsa kuti nkhani yochitila nkhanza anthu a chi albino yazika mizu yoopsa. Apolisi koyamba anamanga munthu ogwila ntchito ya za chipatala mokhudzidwa ndi imfayi.
Wapolisi nayenso anamangidwa mokhudzidwa ndi imfayi. Tsopano wina wanjatwa ndi wansembe wa chikatolika.
A Masambuka anaphedwa mu boma la Mangochi.
Zosakhala bwino kwambiri
Lisiyeni khothi ligwile ncthito yake
Akalangidwa amene achita zoipa pobisalira dzina la mulungu pomati iwo ndi anthu amulungu
Kudako wada ndi mtima omwe eti
amati soka kwa odziwa malemba
Kuchimwa kulibe mwini ngakhale Ansembe amachimwansokulibe mwini
2 Timoteyo 3 verse 1 mpaka 5