Ngati Petulo, a Katolika apotoloka kumukana wa nsembe okhudzidwa ndi kupha

Advertisement
Reverend Father Muhosha

Mpingo wa Katolika mu Diocese ya Zomba watulutsa chikalata choonetsa kukhumudwa ndi wansembe wawo a Thomas Muhosha amene anamangidwa poganizilidwa kuti anatengapo mbali pa imfa ya a Macdonald Masambuka.

Malinga ndi chikalatachi, a Muhosha aimitsidwa tsopano ngati wansembe. Chikalatachi chanenanso kuti Mpingo wa Katolika umalemekeza moyo wa munthu aliyense ndipo supeleka mphamvu yochotsa moyo.

Reverend Father Muhosha
a Muhosha aimitsidwa ngati wansembe.

A Muhosha anjatidwa pamene Apolisi akufufuza anthu amene anapha a Masambuka amene anali munthu wa chi albino.

Imfa ya a Masambuka ndi kafukufuku amene watsatila zaonetsa kuti nkhani yochitila nkhanza anthu a chi albino yazika mizu yoopsa. Apolisi koyamba anamanga munthu ogwila ntchito ya za chipatala mokhudzidwa ndi imfayi.

Wapolisi nayenso anamangidwa mokhudzidwa ndi imfayi. Tsopano wina wanjatwa ndi wansembe wa chikatolika.

A Masambuka anaphedwa mu boma la Mangochi.

Advertisement

7 Comments

Comments are closed.