
Apolisi ku Chileka munzinda wa Blantyre, anjata wonyamula mfuti mzawo pomuganizira kuti adachita nsipu wamera mukhola pa mayi wina yemwe adatsekeledwa mchitokosi cha polisi ya Lunzu.
Usiku wa Lachiwiri laliwisili, Victor Kachingwe, adachita madyera mphoto pa Brenda Lyson wa zaka 20 yemwe adali muunyolo pa mlandu wina. Atalonjezedwa kuti zikatheka amasulidwa, Lyson adadzipeleka kuchita masewero olimbitsa thupi ndi Kachingwe.
Chatsitsa dzaye nchakuti Lachinayi, bwalo la milandu la Chisenjere lagamula Lyson kukaseweza jere zaka zinayi. Apa mpomwe mayiyu adazindikira kuti wagobora opanda dipo. Pakuti wakufa saopa kuwola, Lyson m’maso muli mbee adauza khothilo kuti Kachingwe adamunyengelera kuswa naye mtedza pomulonjeza kuti zikatelo amasulidwa.
Iye anati adali wodabwa akuwuzidwa kuti akaseweza jere pomwe adali atagwira kale ntchito ya kalavula gaga ndi Kachingwe-yo. Munkuthwanima kwa diso, mshomoli Kachingwe adalawa unyolo ndikulowetsedwa mchipinda momwemo momwe adachitira kusawelezikamo.