Nyumba ya Malamulo yadutsitsa ma bill awiri okhudza ngongole

Advertisement
Chithyola Banda

Aphungu a Nyumba ya Malamulo lero adutsitsa bill yoti boma livomeleze ngongole ya ndalama kuchokera ku OPEC for International Development yokwana 20 million dollars yothandizira ntchito za gawo lachiwiri la Shire Valley Transformation Program (SVTP), komanso bill yolora kungongora ndalama ku European Bank zopita ku ma water board m’dziko muno.

Aphunguwa ati ngongolezi ndizopindulira m’Malawi aliyense ngakhale amene sanabadwe. Ma bill-wa anabwera ndi nduna yowona za chuma, a Simplex Chithyola Banda, koma poyankhulapo lero mnyumba ya malamulo mu mzinda wa Lilongwe, oyankhulira chipani cha DPP potsilira ndemanga pa bill-yi, phungu wa dela la Mangochi Monkey-bay a Ralph Jooma wati kufika lero boma langongola koposa kasanu pa nkhani ya SVTP ndipo ati boma libwere poyera kunena chomwe chachitika kufika lero pa ntchitoyi.

A Jooma ati boma liwonetsetse kuti ntchitoyi yatha ncholinga choti zipatso zake ziyambe kuwoneka ndi kuti dziko liyambe kupeza ndalama zakunja likagulitsa zokolora zake kuchokera ku SVTP. Iwo anatinso ogwira ntchito kumaloku akuyenera kugwira ntchito maola 24 kuti ntchito ithe nsanga ndipo phindu liyambe kuwoneka.

Poyankhulira chipani cha UDF, a Lilian Patel Phungu wa kummwela kwa boma la Mangochi, ati pamene nkhani yokhudza Shire Valley Transformation program (SVTP) itabwera mu 2017 aliyense anakondwera powona kuti mavuto anjala ndi chuma atha, koma ati ndi okhumudwa ndi chidodo cha m’mene ntchitoyi ikuyendera.

A Shadreck Namalomba Phungu wa Mangochi South West ati limodzi ndi ku auditor General pakufunikanso kawuniwuni wa m’mene ndalama zopita kuntchotoyi za gawo loyamba zayendera, ndipo ati ndondomekoyi ndi yofunika kwambiri mwakuti boma liganizire kuyambitsanso ku maboma ena.

Bill-yi inadza pofuna kulora unduna wazachuma kubwereka ndalama zokwana 20million za ku America ndi cholinga chofuna kuchulukitsa zokolora kudzera ku ndondomeko ya SVTP yomwe ndi ya zaka 14 ndipo igwiridwa pa ma hekitala 43,000 a malo m’boma la Nsanje ndi Chikwawa poyika zipangizo zamakono zothilira.

Aphuwa adutsitsanso Bill number 31 ya m’chaka cha 2024 yolora boma kutenga ngongole ya ndalama zokwana 90 million Euros kuchokera ku European Investment Bank, ndalama zomwe zipite ku nthambi zogawa madzi m’dziko muno kuti zitukulire ntchito zake ndi kukuza ntchito yawo yogawa madzi ku madera ambiri komanso kufuna kuthana ndi mavuto a madzi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.