Phungu wa Zomba Malosa wadandaula ndikuchedwa kumalizitsa chipatala cha Domasi

Advertisement
Zomba

Phungu wa nyumba yamalamulo m’dera la Zomba Malosa, Grace Kwelepeta, wadandaula ndikuchedwa komalizitsa chipatala cha Domasi chomwe chidayamba kumangidwa zaka zisanu ndi ziwiri zapita mbuyomu.

Kwelepeta wadandaula izi kunyumba yamalamulo ndipo wati kuchedwa kotsekulira chipatalachi kukuphwanya ufulu wa anthu amdera lake lolandira chithandizo chaza umoyo akadwala komanso likuyika miyoyo yawo pachiwopsezo.

Iye wati pakadali pano, chipatalachi palibe magetsi komanso madzi zomwe zikutsonyedza kuti chitenga nthawi chisadayambe kugwira ntchito yake.

“Tipemphe Boma kuti lipange machawi litsekure chipatala cha Domasi ndipo ndine odabwa chifukwa mtsogoleri wadziko lino Dr Lazerus Chakwera atayendera chipatalachi miyezi iwiri yapitayi adalonjeza kuti chipinda chochitira opareshono chiyamba kugwira ntchito pa 1 August koma chodabwitsa kufika lero sadachitsekulire,” iwo anatero.

Koma poyankhapo zapempholo, Nduna ya Zokopa Alendo, Vera Kamtukule yemwe adayankha moyimilira Nduna yaza Umoyo, adati pofika pa 1 September chaka chino chipatalachi chiyamba kugwira ntchito yake.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.