Sitikutulutsa 10,000 Kwacha, yatero RBM

Advertisement

Mkulu wa banki yaiyikulu m’dziko muno ya Reserve, a Wilson Banda, akana zoti bankiyi ikufuna kutulutsa K10,000 yogwirana.

Polakhula ndi atolankhani a Wilson Banda anena kuti Bankiyi ilibeso maganizo otulutsa ndalamayi pakali pano ndipo zomwe zikuyenda masamba a mchezo ndi zabodza ndipo anthu asakhulupirire zimenezo.

Iwo atsindika kuti bankiyi singatulutse ndalamayi chifukwa pakali pano ali pa ntchito yoti akwanilitse ndondomoke zomwe zingathandize kuti ndalama ya Kwacha isagweso.

“Zomwe akufalitsa anthu ena kuti Ife tikufuna titulutse ndalama ya pepala ya K10,000 ndi bodza lankunkhuniza kaamba koti chithunzi chomwe anthu akugawana pa masamba amchezo ndi K10 yakale ndipo angoonjezerapo ma zero pachithunzi cha K10 yakaleyo choncho izi sizikuchokera kwa Ife,”

Malingana ndi a Banda, zomwe zikumvekaso m’masamba a mchezo kuti Bankiyi ikufuna igwetse ndalama ya Kwacha ndi 13 percent ndi zabodza ndipo anthu asakhulupirire zomwe zikumveka masamba a mchezo.

Advertisement