
Timu ya Karonga United yamenya ndi kutulutsa timu ya Mighty Wanderers mu masewelo a quarter final yachiwiri ya chikho cha Airtel Top 8 omwe anachitikira pa bwalo la Karonga.
Wanderers inayamba masewelowa ili ndi chigoli chimodzi mthumba koma chigawo choyamba chinatha osabala kanthu ngakhale ma timu awiriwa anayesetsa kupeza mipata ingapo yomwe sinaphule chigoli.
Pa 55′ captain Pilirani Thulu anasema mpira wabwino omwe unakapeza Alfred Chizinga yemwe sanaphonye kumenya omdutsa Chancy Mtete kutsogoza ng’ona za ku Karonga 1-0 kubweletsa zinthu (1-1) pa aggregate.
Chizinga anabweranso patangotha mphindi 19 pomwe analandira mpira ndi mutu kuchoka kwa Robert Luhanga 2-0, (2-1) pa aggregate.
Wanderers yomwe ndi akatswiri a chikhochi m’chaka cha 2022, anayesetsa kulowetsa Mwalilimo, Kung’unde kuti mwina n’kupeza mwayi kufananitsa mphamvu kuti akhale ndi mpata ndi mwayi komabe masamuwa omwe sanathandize kupulumutsa manoma mkamwa mwa ng’ona za Karonga,
Pakutha pa zonse Masewelo atha 2-0 (2-1) pa kusonkhanitsa zigoli za masewelo onse awiri, ndipo Karonga oyenda tsopano kukakumana ndi FCB Nyasa Big Bullets mu ndime ya ma timu anayi (semifinals).