Phungu wa MCP wapepesa atanena kuti anthu akumudzi sadandaula za mafuta ophikira

Advertisement

,Phungu wa chipani cha MCP kum’mwera kwa boma la Ntchisi, a Ulemu Chilapondwa, apepesa pa zomwe anayankhula dzulo kuti anthu akumudzi sadandaula za kukwera mtengo kwa mafuta ophikira.

A Chilapondwa apepesa lero mu nyumba ya malamulo ku Lilongwe.

Ku nyumba yamalamulo aphungu akukambirana zokhudza ndondomeko ya za chuma ya chaka chino kufika chaka cha mawa.

Dzulo, a Chilapondwa amayankhapo pa zomwe anayankhula mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma m’nyumbayi a Kondwani Nankhumwa omwe lolemba pa 7 February anapempha boma lamgwirizano wa Tonse kuti aganizile bwino zakufunika kotsitsa mitengo ya mafuta ophikira.

A Nankhumwa anati ndizokhumudwitsa kuti boma la Tonse motsogozedwa ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera sakuonetsa chidwi cheni cheni pakukwera mtengo kwa zinthu mdziko muno kuphatikizapo mafuta ophikira.

Koma a Nankhumwa anakwiyitsa a Chilapondwa omwe poyankhapo anati ndiodabwa kuti a Nankhumwa akukamba za zinthu zomwe sizofunika komaso zosapeleka chiyembekezo kweni kweni ku mtundu wa a Malawi.

A Chilapondwa anauza nyumbayi kuti pakadali pano anthu akumudzi akufunikira mayankho kumavuto eni eni omwe awakhuza osati nkhani yakukwera mtengo kwa mafuta ophikira ponena kuti mafuta ophikira ndi a anthu okhala ntawuni okha.

“M’malo mopeleka mayankho kuzinthu zofunikira, mtsogoleri wambali yotsutsa boma akukamba zam’dipiti wagalimoto ya president, akukamba zamafuta ophikira. Nkhani yamafuta ophikira ndiya anthu antawuni osati akumudzi.

“Anthu kumamidzi sakufuna mayankho pa nkhani ya mitengo ya mafuta ophikira, akufuna mayakho pa zinthu zeni zeni zomwe zakhudza miyoyo yawo,” anatero a Chilapondwa.

Mawu a Chilapondwa anakwiyitsa aphungu ochuluka makamaka a mbali yotsutsa boma.

Lero a Chilapondwa apepesa pa zomwe anena ndipo ati amvetsetsa tsopano kuti mafuta ndi ofunikira ophikira kwa aliyense.

Advertisement