A Sean Kampondeni omwe amayankhulira a pulezidenti Lazarus Chakwera ati dziko la Malawi ndi la mabodza ndi miseche komanso muli anthu ena okhulupirira kuti anthu ogwira ntchito m’boma ndi akuba.
A Kampondeni anayankhula izi lolemba ku State House pomwe amayankhapo pa nkhani yoti pali anthu ena ogwira ntchito m’boma oti ali ndi milandu kuti ayankhe koma sakuchotsedwa ntchito.
Iwo anati mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera achotsadi anthu ena ntchito koma motsata malamulo okhudzana ndi kachotsedwe ka anthu pa ntchito.
Iwo anaphatikizapo kunena kuti pena pamakhalanso mabodza chifukwa anthu ena amakhulupirira kuti aliyense ogwira ntchito m’boma ndi wa ziphuphu, kaya wakuba kapena chigawenga.
Malingana ndi a Kampondeni, anthu ena amayembekezera kuti pomwe a Chakwera atenga boma ndiye kuti aliyense amene wagwira ntchito mu boma kwa zaka 25 zapitazi achotsedwa ntchito zomwe sizingakhale za chilungamo.
“Mu dziko mwathu muno timangokayikirana zinthu zambirimbiri. Koma chilungamo kuti chiyende m’dziko pamayenera zinthu ziyende mwadongosolo. Vuto ndi la kuti mwina tili pa changu koma dongosolo limadana ndikupanga zinthu mwaphwanyaphwanya,” anatero a Kampondeni.
Iwo anatsimikizira a Malawi kuti onse ogwira ntchito za boma omwe analakwa awunikiridwa ndipo ma umboni ake apezeka chifukwa a Chakwera apereka mphamvu ku mabungwe a boma a zofufuza milandu.