Kapena Usi akufuna u VP? – Namalomba


Picsart 26 11 17 11 27 50 610- Malawi24

Mwina akadadziwa Michael Usi adakangokhala osapereka maganizo ake pa momwe adindo angathanirane ndi mavuto a zachuma omwe akuta dziko lino, chifukwa nde wangodzikalasulira moto.

Woyankhulira boma yemweso ndi nduna yofalitsa nkhani Shadric Namalomba, wasambwadza Usi, ndipo wamuuza kuti ngati akufuna apatsidweso udindo wa wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko anene.

Chatsitsa dzaye nchakuti Lolemba sabata ino, Usi anachititsa msonkhano wa atolankhani komwe anafotokoza zakuthekera kwake kothandiza boma kuthana ndi ena mwa mavuto omwe akuta dziko lino.

Mwazina, Usi anati ali ndi upangiri omwe ungathandize ulamuliro wa DPP motsogozedwa ndi a Peter Mutharika kuthana ndi vuto la kusowa kwa mafuta a galimoto lomwe lakhala kwa miyezi itatu tsopano.

Koma uku kunali kutokosola mavu nkhomola poti Namalomba walavula zakukhosi.

Namalomba wati ndiodabwa kuti Usi anakanika kuthetsa vuto lakusowa kwa mafuta pa nthawi imene anali wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino ndiye pano akwanitsa bwanji.

Iye wati ndiodabwa kuti Usi waupeza liti ukadaulo umenewu popeza DPP yakhala m’boma chaka chimodzi chokha.

Komabe Namalomba wati akuwathokoza a Usi chifukwa anabwera poyera ndikufotokoza kuti ali ndi kuthekera kofuna kugwira ntchito limodzi ndi boma.

Iwo ati izi zikulingana ndi zina zimene anafotokoza m’tsogoleri wa dziko lino a Mutharika kuti kugwira ntchito limodzi ndichofunikila kusiyana ndi kutsogoza ndale.

“Mmene anafotokozera a Pulesidenti ananena kuti nthawi ino si nthawi ya ndale, ndi nthawi yakuti tonse tigwirane manja tikakonze dziko lino,” adatero a Namalomba.

Komabe a Namalomba adati ndiwodabwa kuti a Usi anayitanitsa m’nsonkhano wa atolankhani kusiya kulumikizana ndi ofesi ya nduna yowona za mphanvu a Jean Mathanga.

“Kodi padalibe njira zina zabwino? kodi kuthetsa mavuto amenewa azikachitikila pa press conference?” wadabwa Namalomba.

Iwo adati zimene achita a Usi zikuwonetseratu kuti amasungira ka mpeni kakuthwa ku mphasa chipani cholamula cha DPP.

A Namalomba adatinso nthawi zina amalumikizana ndi a Usi koma mukucheza kwawo sanayambe afotokozapo zakuthekera kumene alinako kothandiza boma.

Latest vacancies

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading