Inde boma ndichimatchini ndipo chikafuna kuluma sichisewera: Koma kwapano khala ngati manu aguluka. Nalo lalema ndi vuto lakusowa kwa mafuta, mpaka lawuza kampani kuti ziwuyatse ulendo wa kunja zikasake zokha dizilo.
Bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) lati tsopano lipereka chirolezo ku makampani omwe akugwira ntchito zazikulu zachitukuko kuti zipite kuli konse komwe zingathe kukagula mafuta.
M’kalata yomwe yasainidwa ndi mkulu wa bungweli, Dad Chinthambi, MERA yati makampani omwe amagwiritsa ntchito dizilo wambiri atha kupempha chilolezo choti azigula okha mafutawa kuchokera kunja kwa dziko lino.
Komabe, MERA yati makampani omwe akufuna chilolezochi akuyenera kusonyeza kuti ali ndi malo okwanira osungiramo mafuta kapena njira zodalirika zosungira diziloyo mosamala.
Kuwonjezera apo, bungweli lati lisanapereke chirolezochi, lidziyamba lawunika ngati kampanizo ziri ndi zoziyenereza zonse.
Vuto la kusowa kwa mafuta, tsopano liri m’mwezi wachitatu chiyambireni ndipo palibe chisonyezo choti litha posachedwapa.
Izi zikupereka chiopsezo kuti mabizinesi ndi ntchito zosiyanasiyana zipitirira kusachita bwino.







