Nyerere pakatipa zayenda mwa pendapenda pang’ono, koma zimenezo mtsogoleri wake Thom Mpinganjira sizikumukhudza ngakhale pang’ono.
Iye wauza mphunzitsi wa Mighty Wanderers Bob Mpinganjira kuti ngakhale kubwere mvula kapena kuombe dzuwa, FDH Premiership ilowere ku Lali Luban.
Thom wati khumbo lake ndiloti pomwe chaka chamawa chino Wanderers ikhale ikusangalala kuti yakwanitsa zaka 65 chikhazikitsidwireni, idzakhale ndi zikho zoti idzaloze kuphatikizapo FDH Premiership.
“Ndamuwuza Bob kuti zibwana ayi, ndipo wavomereza kuti tikafera mu ground,” watero Mpinganjira.
Mpinganjira watinso ochemelera timuyi asamathamangire kukhumudwa, komanso kunyoza timu pomwe isakuchita bwino koma adzikhala patsogolo kuwalimbikitsa aphunzitsi ndi osewera.
Mtsogoleri yu amayankhula izi pomwe anakayendera ntchito yokonza nyumba ya timuyi (club house) yomwe iri mbali mwa nsewu wa Lali-Lubani ku Chichiri mu mzinda wa Blantyre.
Uko khumutchayu anati pomwe ntchito yokonza Club House yatha, iwo akhale akuyang’ana zomanga bwalo lawo-lawo losewererapo mipikisano kapena kuchitira zokonzekera za timu ponena kuti malo omwe amkati abwereke adakanizidwa.
Pakali pano timu ya Mighty Wanderers iri pa nambala yayichiwiri pa mndandanda wa ma timu a mu mpikisano wa FDH Bank Premiership ndi mapoint 39 kulekana ma point atatu okha ndi FCB Nyasa Big Bullets yomwe iri patsogolo.