Woyimbira akakhalebe omwewa, tisiya mpira – Jomo


Silverladiesjpg- Malawi24
Mwini wake wa timu ya Kukoma Ntopwa Women’s, Isaac Jomo Osman wati zomwe zikuchitika kumbali yamayimbiridwe mu mpikisano wa NBM Women’s Premiership ndizachimidzi ndipo kulibwino matimu agwirizane kusiya kumenya.

Jomo anayankhula izi atatha masewero omaliza a timu yake mu gawo loyamba la mpikisano wa chaka chino pomwe anagonja ndi Ascent Academy ndi zigoli ziwiri kwa du!.

Iye anati mpikisanowu ndi waukulu ndipo ukuyenera kulemekezedwa potengeraso kuti uli ndi wosewera omwe akupita ku World Cup ndi timu ya dziko lino, Scorchers.

“Ndiwauze omwe akuyendetsa mpira kuti zikuchitikazi ndizachimidzi. Sikuti oyimbirawa akumakondera, koma kusadziwa zochita. Zoona adziphunzilira mpikisano waukulu ngati uwu? Zoti muli osewera omwe akupita ku World Cup akudziwa koma?” Anafusa motero Jomo.

Iye anapitiriza kuti: “ubwino wake tamaliza gawo loyamba apapa tikuyenera kukambirana ngati ma timu kuti ngati oyimbira ake akhalebe omwewa, tisamakamenye mpirawo”.

Thom Mkolongo wophunzitsa Ascent Academy, nayeso anadandaula za woyimbira ngakhale timu yake inapambana ndipo anagwirizana ndi Jomo kuti ma timu akufunika akambirane ndi woyendetsa masewerowa.

“Ngati tikudandaula koma tapambana ndie mudziwe kuti woyimbira awa sakudziwa zochita ndie pomwe gawo loyamba latha pakufunika ma timu tiyankhule ndi FAM kuti izi zikonzedwe” anatero Mkolongo.

Izi zikutsatira likukumwe lamadando omwe ophunzitsa akhala akupereka pamapeto pamasewero a mpikisanowu chaka chino.

Ena mwa masewero omwe aphunzitsi adandaula ndi pakati pa Wanderers Queens komaso MK Academy omwe anathera 1-1, mphunzitsi wa Wanderers Thom Kazembe anati woyimbira anapereka penate yosayenera.

FCB Nyasa Big Bullets Women ndi Civil Service Women’s atatha 1-1 wothandizira kuphunzitsa Bullets, Charles Lubani anadandaulaso kuti woyimbira amakondera Civil paziganizo zake.

Nayeso Griffin Spencer wa Chitoliro Heroines anati ndiwokhumudwa ndiwoyimbira pomwe timu yake inagonja ndi FACT Ladies. Spencer anadandaulaso woyimbira pomwe timu yake inafa kwa Silver Strikers Ladies.

Madando akhalabe akuperekedwa pomwe Nkolongo anadandaulaso za woyimbira pomwe timu yake inagonjetsa FCB Nyasa Big Bullets Women’s.

Ngakhale kuchoka pachiyambi ma timu akhala akudandaula koma nkhani za woyimbira zinapitilirabe mpaka mwezi uno wa November pomwe MDF Lioness kudzera mwa mphunzitsi Yohane Fulaye, inati anayikanira chigoli chabwinobwino pomwe inkakumana ndi Civil.

Mwezi wa October, Silver Strikers Ladies anayilipitsa kamba ka mpungwepungwe omwe oyitsatira komaso ena mwa wothandizira kuphunzitsa anachita posawonetsa kukondwa ndi woyimbira pomwe anagonja ndi Civil Service Women 3-2.

Koma poyankhula, mlembi wamkulu wamasewero amiyendo a akazi, Lustica Gondwe anavomera kuti akhala akulandira madando kuchokera ku matimu kuti samakhutitsidwa ndikayimbilidwe.

Gondwe wati bungwe la woyimbira linapeza kuti mavutowa amabwera kamba kogwiritsa ntchito oyimbira oyamba kumene koma ati bungweli lalonjeza kuthana ndimavutowa mchigawo chachiwiri cha mpikisanowu.

Latest vacancies

  • Driver Malawi National Examinations Board (MANEB) · Closes 11 Dec 2026
  • Accountant Malawi National Examinations Board (MANEB) · Closes 11 Dec 2026
  • Internal Auditor Malawi National Examinations Board (MANEB) · Closes 11 Dec 2026
  • Chief Executive Officer NICO Asset Managers Limited · Closes 18 Dec 2026
  • Technical Advisor Nutrition International · Closes 7 Dec 2026

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading