Tikapangana kuti tidye galu, timadya ndi mutu omwe – Kabwila


Img 20261005 Wa0015- Malawi24
Mneneli wa chipani cha MCP, Jessie Kabwila wati malamulo a chipanichi anapanga okha ndipo ndipo ali ndi mphamvu zopangana kuti Lazarus Chakwera adzayimire chipanichi pa chisankho cha 2030.

Kabwila amayankha atafusidwa ngati Chakwera akuloledwa kuyimira chipanichi pomwe otsatira ena chipanichi akutsutsana ndi ganizoli.

Iwo ati Lazarus Chakwera anachita zinthu zapamwamba pomwe ankalamulira dziko lino, zomwe a Kabwila akuwona kuti ndiwoyenera pa mpandowu.

“A Chakwera sakuyenera kuyimira mu 2030 ngati angadzagonje chisankho cha mchipani chathu. Ku kongeresi tikangopangana kuti tikudya galu, timadya ndi mutu omwe. Malamulo tinalemba tokha ndipo tili ndi ufulu osankha munthu yemwe angatipambanitse” anatero Kabwila.

Iwo anatchula zinthu ngati magetsi, madzi, mafuta ngati zomwe ati zinkayenda bwino mu nthawi ya a Chakwera, ndipo ati ameneyu ndiye mtsogoleri yemwe a Malawi akufuna.

Kabwila anadzudzulaso ulamuliro wa DPP ponena kuti walephera kuyendetsa dziko lino pa nkhani yakusowa kwa mafuta ndi ndalama zakunja.

Iwo ati mmene zafikira zinthu, mtsogoleri wa dziko lino akuyenera kubwera poyera ndikupereka ndondomeko zomwe boma likupanga pofuna kuthana ndi mavuto omwe alipo pano.

Kabwila anatiso nduna yazamphamvu zamagetsi ikuyenera kutula pansi udindo kamba koti sakudziwa kalikonse kokhudzana ndi udindo wake.

Latest vacancies

  • Driver Malawi National Examinations Board (MANEB) · Closes 11 Dec 2026
  • Accountant Malawi National Examinations Board (MANEB) · Closes 11 Dec 2026
  • Internal Auditor Malawi National Examinations Board (MANEB) · Closes 11 Dec 2026
  • Chief Executive Officer NICO Asset Managers Limited · Closes 18 Dec 2026
  • Technical Advisor Nutrition International · Closes 7 Dec 2026

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading