DPP sikuyenera kukawona nawo mu system ya MEC – Mpekasambo

Advertisement
Mpekasambo

A Kelvin Mpekasambo m’modzi mwa omwe amakhala pa pologamu ya pa Malawi Broadcasting Corporation (MBC) ya Timvetse, ati Malawi Electoral Commission (MEC), isalole chipani cha Democratic Progressive (DPP) kukalowa nawo mu nkhokwe (system ) ya bungwe loyendetsa chisankho la MEC ponena kuti DPP inawonetsa kale m’chitidwe osokoneza masankho a 2019.

Poyankhula a Mpekasambo ati bwalo la milandu lidagamula kuti chipani cha DPP chidabera masankho pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana kotelo palibe chifukwa cholora omwe adagamulidwa kuti adabera akalowe mu nkhokwe (system) ya Malawi Electoral Commission (MEC).

Iwo ati DPP ndi yomwe ikutsogolera kusokoneza anthu kuti adane ndi ndondomeko ya tsopano yomwe MEC ikugwiritsa ntchito ya Smartmatic, ponena kuti ati chipanicho chikusowa polowera kuti chisokoneze.

Pologalamu ya Timvetseyi inayitananso mkulu wa bungwe la Malawi Broadcasting Corporation (MBC), a Humphrey Mvula komanso a Mpekasambo.

Zipani zisanu zidalembera bungwe loyendetsa zisankho la MEC kuti zikufuna zichite kawuniwuni wa zomwe zili mu nkhokwe (system) ya bungwe la MEC masankho asanachitike pomwe kalembera komanso kuwunika mayina m’kawundura kudatha.

Bungweli la MEC kudzera mwa mkulu wa bungweli a Andrew Mpesi, ati bungweli lipeleka chitsogolo cha pempho la zipani zisanuzi posachedwa.

Zipani za Democratic Progressive (DPP), Alliance for Democracy (AFORD), United Democratic Front (UDF), People’s Party ndi United Transformation Movement (UTM) ndi zomwe zinapeleka kalata ku bungweli pa za malire (scope) a momwe iwo akufunira kupanga kawuniwuni mu mkhokwe ya MEC yomwe imagwiritsa ntchito Election Management System (EMD).

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.