M’madera am’mphepete mwa nyanja ya Malawi madzi akhonza kusefukira – DCCMS

Advertisement
Lake Malawi Floods

Nthambi yoona zanyengo m’dziko muno ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yachenjeza anthu okhala m’mphepete mwa Nyanja ya Malawi kuti chiopsezo cha kusefukira kwa madzi kwadzidzidzi kukhonza kukwera.

Kudzera pa tsamba lake la m’chezo, nthambiyi yati madera omwe ali pa chiopsezochi ndi monga Nkhatabay ndi Karonga.

“Chiopsezo cha kusefukira kwa madzi mwadzidzidzi chikwera m’madera am’mphepete mwa nyanja ya Malawi monga ku Nkhatabay ndi ku Karonga makamaka kuyambira Lachisanu, pa 18 April 2025. Komanso Mphepo ya Mwera ikuyembekezeka kuomba pa nyanja ya Malawi ndi pa nyanja zathu zina kuyambira usiku wa pa 17 April, 2025. Choncho, tikhale tcheru,” yatero DCCMS.

Nthambiyi yati lero tiyembekezere nyengo ya mphepo komanso mvula ya mabingu m’madera ochuluka ndipo Loweruka sabata ino kudzakhala kwa mphepo ya Mwera komanso kwa mvula.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.