Khansala Willy M’manga aikidwa m’manda

Advertisement
Khansala Willy M'manga

Kunali khamu la anthu ndi nkhope zakugwa komanso zodzala ndi chisoni dzulo pomwe amapelekeza kukayika m’manda thupi la Willy M’manga yemwe anali khansala wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) wa dera la Naming’azi mu dera la phungu la Zomba Malosa,

Khansala M’manga omwe anali otsiliza kubadwa m’banja la ana khumi ndi m’modzi (11) ayikidwa m’manda kumudzi kwawo kwa Kumtamba dera la mfumu yayikulu Malemia m’boma la Zomba.

Willy M'manga funeral

Pa kulira kwawo a Acklen Kanani kuyimira unduna wa maboma ang’ono anati ndi zolilitsa kuti dziko likumataya anthu ndi adindo ochilimika pa ntchito zomwe zikutukula madera, apo ndi pomwe anati khansala M’manga anali odalilika.

Mfumu yayikulu Malemia ya m’boma la Zomba inati inali yosweka mtima kumva kuti khansalayu wamwalira pomwe ku m’mawa wa tsiku Lachisanu lomwe adamwalira, awiriwa adalumikizana kufunsana za moyo.

Iwo anati a M’manga anali chitsanzo chabwino mu dera lawo komanso kuposera dera lawo ndipo ati anali odzichepetsa.

Phungu wa dera la Zomba Malosa, Grace Kwelepeta anati ali ndi chisoni chodzadza ponena kuti zikadakhala bwino akadamalizira limodzi telemu yawo yoyamba ya ntchito, pomwe ati chichokeleni 2019 pomwe khansalayu adasankhidwa, wakhala munthu odalilika kwambiri.

A Thokozani Moyo omwe amayimila Malawi Local Government Association (MALGA), apempha ma khansala kuti adzikhala ofikilika komanso odzichepetsa nthawi zonse monga analili khansala M’manga

A Moyo anapemphanso mwapadera kuti nthawi yakwana tsopano kuti mayendedwe a ma khansala awunikidwebe, kuphatikiza chisamaliro chawo pomwe ati imfa zina za ma khansala zachulukira ndi za ngozi ya njinga zamoto.

Iwo anati mwa makhansala 13 omwe amwalira tsopano, kuposa theka la iwo anamwalira chifukwa cha ngozi za njinga.

Khansala M’manga adamwalira Lachisanu atadwala kwa nthawi yochepa nthenda ya kukwera kwa shuga, ndipo alowa m’manda ali ndi zaka 52. Iwo asiya mkazi ana asanu ndi atatu (8) ndi zidzukulu ziwiri.

Ku mwambowu kunafika aphungu a kunyumba ya malamulo oposa asanu, bwanamkubwa wa boma la Zomba , mfumu ya mzinda wa Zomba ndi adindo ena.