
Nkhondo ya masewelo a mpira wa miyendo yomwe inalipo Loweluka lathali pakati pa Silver Strikers ndi Mighty Wanderers mu mpikisano wa 2025 NBS Bank Charity Shield yakwanitsa kupanga ndalama zokwana 66.8 million Kwacha, masewelo omwe anaphopholika mu mzinda wa Lilongwe.
Malinga ndi bungwe la Football Association of Malawi (FAM), mu masewelowa 61.7 million yapezeka kudzera ku ma tikiti omwe anthu anagula, 5.1 million yapezeka kuchokera ku nyumba zofalitsa nkhani pomwe pamwamba pake panali kale 60 million Kwacha ya thandizo kuchokera ku bank ya NBS kufikitsa ndalama zonse zopezeka pa 126.8 million Kwacha.
FAM yati mpikisano wa chaka chino ndalama zake zaposa ndi theka la zomwe zinapezeka mu mpikisano wa ngat omwewu wa mchaka chatha cha 2024 pomwe ndalama zokwana 43.6 million ndi zomwe zinapezeka.
FAM yati pa ndalama zonse zomwe yatolera, ndalama zokwana 61.1 million ndi zomwe zinagwiritsidwa ntchito kulipilira achitetezo, bwalo, kufalitsa ma uthenga, ma tikiti ndi zina zambiri.
Mtsogoleri wa bungwe la FAM, a Fleewood Haiya wayamika NBS bank pokweza thandizo lake kuchoka pa 40 million kufika pa 60 million, ndipo wathokoza anthu omwe anafika kudzaonera masewelowa komanso kudzathandiza poti masewelowa ndi a chifundo.
Timu ya Silver Strikers idaswa Mighty Wanderers kudzera pa ma penate pomwe inachita kuchokera kumbuyo kukafananitsa mphamvu kuti masewelowa athere 2-2 pa mphindi zonse za m’bwalo zokwana 90 ndipo zigoli za Wanderers zinachoka kwa Sama Thierry Tanjong ndi Blessings Singini pomwe ma Banker adabweza kudzera mwa Binwell Katinji ndi Zebron Kalima.
Ataseweledwa ma penate timu ya Manoma yomwe inamenya chikhochi chifukwa chopambana chikho cha 2024 Castel Challenge, inabwelera kwawo ku Lali Lubani itagonga 5-3 kupanga akatswiri a 2024 TNM Super League kutenganso 2025 Charity Shield.