
“Khaaa kuti khaaa..”Julius Mithi apata shuwa pomwe ma loya odziwika bwino mdziko muno a Silvester Ayuba James ndi a Khwima Mchizi ati akayimilira mwa ulele a Mithi omwe awamanga dzulo mu mzinda wa Mzuzu.
A Ayuba James omwe alemba nkhani yokhudza kuyimila a Mithi mwaulele pa tsamba lawo la mchezo la Facebook, pomwe anapita kukacheza ndi a Mithi ku polisi komwe akuwasunga kudikira tsiku la milandu yawo.
“Khwima and I are giving him pro-bono representation. We just had a very spirited chat this morning at his police cell. (Khwima ndi ine tikuwaimilira mwa ulele. Tinacheza nawo kum’mawaku ku chitolokosi cha apolice komwe ali),” analemba motelo mchizungu.
A Mithi omwe akuwasunga ku polisi ya Kanengo ndipo ndi odziwika bwino maka pa tsamba la mchezo la Facebook, anawamanga chifukwa cholemba pa tsamba lawo pa 19 March 2025, pomwe anati mayina a anthu omwe analembetsa voti oposa 1 million anafutidwa mu mphika wa bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) ndi bungwe lolemba za unzika la National Registration Bureau (NRB).
M’modzi mwa oyimira a Mithi pa mulandu, Khwima Mchizi poyankhula ndi nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno wati a Mithi akawonekera kubwalo la milandu mawa.
M’neneli wa apolisi mdziko muno a Peter Kalaya anati mabungwe awiriwa omwe ndi a MEC ndi NRB adakamang’ala ku polisi pa zomwe a Mithi analemba ndi chifukwa chake anawamanga.
A Julius Zawanda Mithi amadziwika kwambiri ndi kudzudzula mbali yaboma pa zinthu zosiyanasiya zomwe zachitika mdziko muno.