
Timu ya mpira wa miyendo ya Malawi the Flames’ yaswa timu ya South Africa ndi chigoli chimodzi kwa duu pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.
Masewelo a mu gawo lachiwiri (Round 2 ) ya African Nations Championship CHAN Malawi yamwemwetera mu chigoli chochoka kwa Zeliet Nkhoma pa mphindi ya 87.
Kalisto Pasuwa anadalira koyamba ntchito za George Chikooka pa golo, MacDonald Lameck, Maxwell Paipi, Lloyd Aaron, Nickson Mwase, Yankho Singo, Gaddie Chirwa, Binwell Katinji, Alick Lungu, Zeliet Nkhoma ndi Wisdom Mpinganjira.
Chigawo choyamba chinatha opanda chipatso ngakhale njala inali kwa Malawi kufuna kupeza chigoli Koma Bafana Bafana inakunga Khoma kumbuyo.
Pa mphindi ya 62 Pasuwa anatulutaa Yankho Singo ndi Binwell Katinji kulowetsa Olson Kanjira ndi Chawanangwa Gumbo kuti mwina mphatso ya chigoli mkupezeka.
Koma ntchito za osewera wa Mighty Wanderers Wisdom Mpinganjira yemwe anawonetsa kuchilimika lero, zinawonekera pa mphindi ya 87 pomwe anasema mpira kudzera pa kona ndi kukapeza mutu wa Zeliet Nkhoma mu ukonde KHWEEEETCHEEEE!!! 1-0
Mphindi zinayi zowonjezera sizinaphule mwayi kwa anyamata a South Africa, apa Malawi ikuyembekezera kukamuna ndi Bafana Bafana-yi mu masewela a chibweleza mu mzinda wa Pretoria kuti ngati ingakapambane pa 11 pano ndekuti adzigulira malo ku masewelo omaliza amene akakhalepo ku Kenya,Tanzania ndi Uganda mu Mpikisano wa CHAN.
Kalisto Pasuwa anawuziratu anyamata ake asanayambe masewelowa kuti akuyenera kukasewera ndi mphamvu zonse, kudzipeleka mpaka akapeze zotsatira zolongosoka.