
Maganizo a Malawi24 monga m’mene alilinso a aMalawi ena okhudzidwa, ndi okonda dziko lawo, tikanakonda kuti boma lidzichalira pomanga zitukuko zake zina. Ndi zomvetsa chisoni ndi zowawa kuti ndalama zoposa 4 billion Kwacha zikanatha kupulumuka pa ntchito yomanga nyumba ya mabwalo a milandu ya High Court-Commercial Division Registry mu mzinda Blantyre, yomwe imayenera kutha mzaka ziwiri koma yatha zaka 15.
Ntchito yomwe inayamba pa 16 August 2010 inayelekezedwa kutha mzaka ziwiri ndi ndalama zokwana 1.2 billion kwacha, koma yatha zaka 15, ndipo pomwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera amakatsekulira yadya ndalama pafupifupi 5.2 billion Kwacha, izi ndi malingana ndi mkulu wa mabwalo a milandu, Justice Rizine Mzikamanda SC.

Ntchito yomanga Commercial court yomwe ndalama zake zonse zinali zochokera ku boma la Malawi, kukakhala chete ndi kuganiza ndalama zokwana 4 billion Kwacha kuchoka ku misonkho ya a Nambewe ku Ntcheu, A Namtchathu ku Balaka, A Zimba ku Karonga, a Paipi ku Mangochi mwa ena, mzika itha kuwona chidodo cha ndithu cha kayendedwe ka ndondomeko ndi zinthu m’dziko lathu maka ku boma.
Monga mu mawu a m’modzi mwa oyimila anthu pa milandu Khumbo Soko yemwe analemba pa tsamba lake la mchezo, anati tikuyenera kukhala serious ngati dziko, pomwe wati nyumba yosanjikizana chabe kasanu mpaka yatha zaka 15.
“Atsogoleri a dziko anayi adutsa, atsogoleri a ma bwalo a milandu atatu, anthu kuyamba chibwezi kumanga banja kubeleka mwana oti pano ali ndi zaka 12? Nadi mwewathu?” anatelo a Soko.
Malawi24 yawona kuti Ichi ndi chitsanzo cha kusakazika kwa chuma mu zina mwa zitukuko zomwe pakali pano zinayima kapena zikuyenda ngati liwilo la nkhono monga kumanga sukulu, zipatala mwa zina, mabwalo a Mpira mwachitsanzo la Zomba lomwe linayamba pafupifupi khumi zapitazo.
Tikayelekeza ndalama zokwana 4 billion zomwe zasakazika chifukwa cha chidodo, ndi kuchepa kwa chindunji, ndalamazi zikanatha kugwira ntchito mu nthambi zina zinayi kapena zisanu zaboma mu ndondomeko ya zachuma cha thunthu mwachitsanzo 2025/2026 yomwe aphungu anadutsitsa.
Mwachitsanzo mu ndondomeko ya zachuma yomwe nduna Simplex Chithyola Banda inapelela; 4 billion Kwacha ya pamwambayi ikanatha kugawidwa kupita ku National Local Government Finance Committee yomwe inapatsidwa 1.101 billion Kwacha, Civil Service Commission yomwe inapatsidwa 1.4 billion, Independent Complaints Commission yomwe inapatsidwa 1.44 billion, Attorney General’s yomwe inapatsidwa 964 million ndi National Intelligence Services Complaints Tribunal yomwe inapatsidwa 415.1 million mu 2025/2026.
Justice Mzikamanda popeleka mbiri ya ntchitoyi pomwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera amakatsekulira mnyumbayi lachitatu masana anati;
- Ndalama zonse zomangira nyumbayi nzochoka ku boma la Malawi
- Malawi High Court Commercial division inayamba pa 14 May 2007 ndipo ma office ake anali mu nyumba zobweleka za MPICO momwenso anawatulutsamo
- Ntchito yoyamba kumanga nyumbayi inayamba pa 16 August 2010,
- Ntchitoyi imayembekezeka kutha pofika pa 21 September 2012
- Ndalama zokwana 1.2 billion zinayikidwa zomalizira ntchitoyi
- Ndalamazi zinakula kufika pa 2.7 billion pofika 8 December 2016
- Ndipo zinakulanso kufika pa 4.1 billion pofika May 2018
- 5.1 billion kwacha pofika mchaka cha 2022
- Pafupifupi dzaka 15 kufika pano
- 5.2 kapena kuposera apo ndi yomwe ikuganizilidwa kuti yatha,poti kuwelengera kuli mkatibe
- Ikanatha mwamsanga ntchito yomangayi, nthawi ikanasamalidwa komanso ndalama ikanasamalidwa.
Ife ngati Nyumba yofalitsa nkhani tikuti tiyeni ngati dziko tidziphunzirapo, ndi kumva Chisoni ndi chidodo komanso kusakazika kwa ndalama za aMalawi zomwe zikanatha kusamalika.
-Dziwani izi ngati inu adindo ndalama sikuvutani kupanga, Koma aMalawi ambiri ndalama amayisaukira kuti ayipeze kuti MRA idzadule misonkho.