
Bambo wa zaka 42, James Kaipa, ali mchitokosi cha apolisi ku Balaka pomuganizira kuti anapezeka ndi mfuti popanda chilolezo.
M’neneri wa apolisi m’bomali, Inspector Gladson M’bumpha, wati Kaipa adagwidwa ndi apolisi m’dera la Phalula pamodzi ndi anthu ena anayi omwenso akuyankha milandu yosiyanasiyana.

A M’bumpha ati Kaipa akawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mulandu opezeka ndi mfuti popanda chilolezo pomwe oganizilidwa enawo akayankha milandu monga yogwililira, kuthyola nyumba komanso kuwotcha katundu wa eni mwadala.