Gaba ndi Petro atsala pomwe Flames yanyamuka wa ku Tunisia

Advertisement
Gaba

Timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino ya the Flames yanyamuka ulendo wokakumana ndi Tunisia m’masewelo olimbirana malo ku mpikisano wa 2026 FIFA World Cup kudzera pa bwalo la ndenge la Kamuzu international mu nzinda wa Lilongwe, pomwe yanyamuka opanda Frank Gabadinho Mhango ndi otseka kumbuyo Charles Petro omwe ndi ovulala.

Pa ulendo wake Flames idutsira ku Johannesburg, mdziko la South Africa kuti ikalumikize ulendo wake okasewele ndi Tunisia Lolemba mdziko lawo.

Flames usiku wa dzulo inali ndi masewelo ake omwe yagonja ndi Namibia ndi chigoli chimodzi kwa du (0-1) pa bwalo la Bingu mu nzinda wa Lilongwe.

Prins Tjiueza ndi yemwe analanga Malawi pa mphindi ya chi 41 m’chigawo choyamba, ngakhale Flames, inawoneka ili ndi njala yofuna chigoli m’chigawo chachiwiri, masewelowa Namibia inatolerabe ma points onse atatu pakutha pa mphindi zonse 90+4.

Osewela onse omwe anyamuka;

Otchinga Pagolo
William Thole
George Chikooka
Richard Chimbamba

Otchinga kumbuyo
McDonald Lameck
Alick Lungu
Nickson Mwase
Gomezgani Chirwa
Nickson Nyasulu
Maxwell Paipi
Dennis Chembezi
Precious Sambani

Osewera pakati
Yankho Singo
John Banda
Patrick Mwaungulu
Lloyd Aaron
Lanjesi Nkhoma
Lloyd Njaliwa
Wisdom Mpinganjira
Zebron Kalima
Gaddie Chirwa

Ogoletsa
Richard Mbuli
Chawanangwa Kaonga
Ephraim Kondowe