Waphwanyitsa sukulu kamba kofuna kukhala m’phuzitsi wamkulu

Advertisement
Emchakachakeni CDSS

Mawu oti agalatiya mwataya chipangano apherezera pa sukulu ya sekondale yoyendera ya Emchakachakeni m’boma la Mzimba pomwe m’phunzitsi wina yemwe akuti anamema ana kuti achite ziwonetsero zokwiya ndi m’phunzitsi wa mkulu pasukuluyi amugwira pakhosi.

Malipoti ati a Flemings Chimawaka, anamemeza ophunzira pasukuluyi kuti aphwanye sukuluyo ndicholinga chakuti iwo adzakhale m’phunzitsi wamkulu ngati yemwe alipoyo atamusamutsa pasukulupa ndipo iwo analonjeza anawo kuti adzasangalara iwo akadzakhala pa mpandowo pomapita muma ulendo ambirimbiri.

Pa 18 February chaka chomwechino, anawo anachita monga mwapangano ndi m’phunzitsiyo ndipo zinathekadi.

Koma paja amati m’dya nyemba amayiwala pomwe mtaya makoko sayiwala, a Chimawaka atakhara pampandowu, anatulutsa zibaluwa zoyimitsa sukulu ana khumi ndi atatu (13) ponena kuti ndi omwe anatsogolera anzawo kuononga sukuluyo, kuyiwala kuti ndi iwo omwe anawatuma anawo.

Pakadalipano ophunzirawo atemetsa nkhwangwa pa mwala kuti iwo sangathamangitsidwe pasukulupo pomwe adachita chotumidwa kuchita upowo.

“Ife sitingachotsedwe sukulu iwo a Chimawaka ndiwomwe amapanga zokambirana ndi ife kuti tiphwanye sukulu kuti iwo akhala m’phuzitsi wamkulu ndipo pano zawayendera, nde akutichotsa sukulu? sitilora akunama amenewa,” ena mwa anawo anatero.

Malinga ndi zomwe tapeza, a Chimawaka akumveka akulangiza ophunzira kuti achite chiwawa.

 “Mukuchedwa kwambiri. Ophunzira a pa Chifira CDSS ku Nkhata-Bay anawononga sukulu yawo pogwiritsa ntchito pulani ndikukuwuzani panoyi ndipo mudzasangalara ndikadzakhala mkulu wa sukulu,” mawuwo akumveka motero.

Koma a Chimawaka akana kuti adamena ophunzirawo kuchita zamtopola ponena kuti, “Sindikukumbukira kuti ndi liti ndinamemeza ophunzirawo kuchita ziwonetsero. Zikuoneka kuti pali anthu amene akufuna kuyipitsa mbiri yanga. Ndipo rekodi ya mawu ndikotheka kuti anawo anachita kujambula mau anga moyelekeza,” anatero.

Poyankhulapo pankhaniyi komiti ya sukuluyi yati;

“Tidagwirizana kuti palibe ophunzira yemwe achotsedwe sukulu, m’malo mwake, tinati anawo alipire MK16,000 kuti tikonzele zomwe zinawonongeka zomwe makolo onse anavomeleza koma tadabwa kuti awapatsa zibaluwa ana omwe akuyembekezereka kulemba mayeso.

Pakadali pano, makolo ndi anthu a mderari akufuna kuti akuluakulu azamaphunziro asamutse m’phunzitsiyo pa sukulupo kamba kakuti wawonetse khalidwe loyipa.

“Sitikuyembekezera mphunzitsi kulimbikitsa ophunzira kuwononga katundu wa sukulu. Tikufuna achoke,” adatero akomiti ya sukuluyo.