
Bwalo la milandu la Lilongwe Senior Resident Magistrate lalamura sing’anga wa zaka 32, Thomson Benson kuti akagwire ntchito yakalavuragaga kundende kwa zaka 21 pokhuthula zilakolako zake zosakhala bwino pa malo olakwika (pa mwana omupeza).
Superintendent Evance Kantukule anawuza khothi kuti ng’angayu amachita mpakulo pa malo osayenerera, ndipo wakhala akuchita zogonanazi ndi mwana wake wopezayu kuyambira chaka cha 2023.
Ng’angayu akafuna kukhuthula zilakolako zake pa mwana wopezayu amatumiza mkazi wache kumunda nthawi ya dzinja kufuna kuti achite mpakulo modekha mopanda omusokoneza.
Mwezi wa February mwana wopezayu anazindikira kuti ali ndi mimba ya bambo akewa, ndipo anawuza mayi ake omwe anakanena za nkhaniyi ku Polisi ya area 24. Kutsatira kunenezedwaku ng’angayi ananjatidwa.
Popeleka chigamulo chake Senior Resident Magistrate Blacios Kondowe analamura kuti ng’anga yoyenda ili m’manjayi ikakhale kundende zaka 21 chifukwa zomwe inachitazo zosayenera komanso zophwanya malamulo a dziko lino.
Thomson Benson amachokera m’mudzi mwa Khoswe, mfumu yayikulu Kalolo m’boma la Lilongwe.