
Anthu okhala ku dera la Ndirande mu nzinda wa Blantyre ali wefuwefu kusaka madzi odzithira ku nkhope pomwe apolisi akuphulitsa utsi okhetsa misozi ku makomo kwa anthu.
Anthu ena adandaulira apolisi kuti ayesetse kupeza njira zina zothamangitsira anthu omwe akuchita ziwonetselozi, poti utsiwu ukufika ku makomo ndipo ati pafupi ndi msika wa Ndirande pali chipatala cha boma komwe kuli anthu omwe akulandira thandizo la mankhwala.
M’modzi mwa akuluakulu a mu nsika wa Ndirande a Chancy Widon ati anayimitsa ziwonetselo zomwe zikuchitika lerozi ndipo ati pakuwoneka kuti pali kusamvetsetsana kamba koti ati chikalata cha madando awo akapeleka lachiwiri sabata ya mawa kwa bwanankubwa, pomwe ati tsikuli nde lovomelezeka la ziwonetselo.
Anthu ena omwe akutsogolera zionetselo za lero ati akupanga ziwonetselo chifukwa akukayikira kuti akuluakulu ena ku derali adya chitseka pakamwa, koma ati iwo akupanga ziwonetselo ndi cholinga choti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera awonenso kuti zinthu sizili bwino ku Malawi.