
Ochita malonda ku Ndirande mu nzinda wa Blantyre alengeza kuti mawa achita ziwonetsero posakondwa ndi kukwera mitengo kwa katundu osiyanasiyana zomwe akuti zakhuda malonda awo.
Wapampando wa ochita malonda mu nsikawu, Chancy Widon, wauza nyumba zina zofalitsa nkhani kuti iwo akhala akukapeleka madandaulo awo ku khonsolo ya mnzinda wa Blantyre komwenso akakumane ndi bwanamkubwa wa bomali.
“Ndalama zogwiritsa ntchito pa moyo wa munthu zafika pamlingo wosayerekezeka. Pali malonjezo osakwaniritsidwa, monga kumanga mlatho wa Nasolo, adindo akuyenera akatipatse mayankho mawa,” watelo Widon.
Iwo alonjeza kuti ziwonetserozi zikakhala za bata ndi mtendere. Izi zikubwera pomwe lero apolisi alepheretsa ochita malonda ku Limbe kukapeleka nkhawa zawo kwa adindo pa vuto lomweli.