
Mtsogoleri wachipani cha Alliance for Democracy (AFORD), Enock Chihana wati satekeseka ngakhale kuti anthu ena akukonza chiwembu chofuna kuchotsa moyo wawo komanso ena ochita nawo ndale.
Chihana wayankhula izi pomwe anthu ena omwe sakudziwika agenda m’dipiti wa galimoto zomwe iye pamodzi ndi akuluakulu ena achipanichi adakwera lero Lachinayi. Malinga ndi kanema wina yemwe anthu akugawana m’masamba anchezo, izi zachitika ku Mchesi pomwe anthuwa amachokera ku maliro ku Area 24.

Mukanemayo, Chihana wachenjeza kuti khalidweli ndilotsutsana ndifundo za dimokalasi. Iye wati akudziwa kuti akusakidwa koma wanenetsa kuti sawopa.
“Ndimafuna ndiwauze aMalawi kuti ili ndilo dziko lomwe MCP yaganiza kuti tikhale,” watelo Chihana. “Mmene tikupita kuchisankhomu akufuna ndithu wina aphedwenso, ndiye tikudziwa kuti enafe ndife ma target koma sitikuopa. Ifeyo tili nganganga komanso bomali titenga pa 16 September. Kaya aphapo m’modzi kaya awiri koma amene afikeyo dzikoli atenga.”
Chihana wati pakadali pano iwo anapita ku polisi komwe akasiya dandaula, ndipo akuti akhala akudikilira kuti awone chomwe apolisi achite pa dandaulo lawoli. Iwo ati posachedwa achititsa nsonkhano wa atolankhani kuti akatambasule za nkhaniyi.