
Ngati njira imodzi yofuna kuthana ndi ngozi za pa nsewu, a polisi ku Lilongwe alanda njinga za moto zokwana 62 atapeza kuti eni ake a njingazi amaphwanya malamulo a pa nsewu.
Malingana ndi M’neneli wa polisi ya Lilongwe, Inspector Hastings Chigalu wati kamba kakuchukuka kwa malipoti a ngozi za pa nsewu makamaka za njinga za moto zomwe zili pafupifupi 30 pa mwezi, a polisiwa adaganiza zolanda njingazi.
A Chigalu ati ena mwa malamulo omwe eni njingazi amaphwanya ndi kuyenda opanda zipewa zodzitetezera komanso kutenga anthu ochuluka.
Iwo atsindika kuti apolisi apitiliza kulanda njingazi kwa anthu omwe sakutsata malamulo kudzera ku nthambi yake yoona za pa nsewu.