Thumba la chimanga lafika pa 100,000 kwacha

Advertisement
Malawi hunger food crisis

A Malawi akungoyenera kuvala zilimbe pomwe thumba la chimanga la 50Kg lafika pa 100,000 kwacha pa misika ina.

Ku madera ena monga Nchalo, Chikwawa ndi Bangula m’boma la Nsanje anthu akugula chimanga 1800 kwacha pa kilo zomwe zikutanthauza kuti thumba la 50 kg ndi (K90,000). Ku Liwonde, Machinga ndi kwa Manase ku Blantyre ka pelo ka 5 litres kakugulitsidwa pa mtengo wa 10,000 kwacha, zomwe zikutanthauza kuti thumba la 50kg ndi K100,000.

Mtengo wa thumba la chimanga la 50kg ku Karonga ndi K75, 000, ku Nkhatabay ndi ku Salima thumba liri pa mtengo wa 85,000 kwacha, pomwe ku Lilongwe thumba la chimanga ndi K85,000 pena K90,000.

Kukwera kwa chimanga kwadza chifukwa cha kupitilira kwa kugwa mphamvu ya ndalama ya kwacha. Pano njala madera ambiri yafika posautsa ndipo aMalawi ambiri akumagona osadya kalikonse.

Lachisanu m’tsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera anapeleka SONA ku Nyumba ya Malamulo koma chodabwitsa ndi chakuti m’tsogoleri yu sanakambeko zokhudza njala yomwe yavuta m’dziko muno.

Anthu ambiri amayembekezera kuti a Chakwera mu SONA yawo afotokoza njira zomwe boma lawo layika kuti athane ndi njala koma ayi ndithu chete chete, iwo sadakambeko za njala.