
Archbishop wa mpingo wa Katolika mu Archdiocese ya Blantyre, a Thomas Luke Msusa ati chaka chino pokhala chaka cha masankho aMalawi akhalebe aMalawi ndipo alimbane ndi kuchotsa njala ndi umphawi zomwe zakuta dziko lino.
Poyankhula kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo pa mwambo wa maliro a yemwe anali kazembe wakale Lucius Chikuni yemwenso anali katswiri pa ntchito za pa wailesi, a Msusa apempha boma kuti lilole kuti anthu adzasankhe mtsogoleri yemwe akufuna pa masankho amene akubwerawa.
A Msusa atinso ndalama za ma thandizo a kunja zikabwera ku Malawi ena asamapakule kuposa anzawo. Iwo anafunsa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko a Michael Usi kuti “Bwanji odya za enawa simukuwamanga bwanji?”