113 million Kwacha pa masewelo a Silver ndi Bullets

Advertisement
TNM Super League

Bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe lero lakwanitsa kutulutsa ndalama za nkhani-nkhani zokwana 113 million Kwacha kuchokera mu masewelo amodzi a Silver Strikers ndi FCB Nyasa Big Bullets.

Masewelowa omwe anali otsekulira season ya 2025 ya mpikisano wa TNM Super League, apanga mbiri pomwe chitsekulireni bwaloli m’chaka cha 2017 izi sizidachitikepo.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa bungwe la Super League of Malawi (SULOM), a Ronald Chiwawula wayamika khamu la anthu lomwe linabwera pa Bingu kudzawonela mwambo otsekulira League.

A Chiwawula ati izi zikuphelezera zifukwa zomwe bungweli linakanila bwalo la Silver kusankha bwalo la Bingu National.

Babatunde Adepoju ndi yemwe wachitila chipongwe akatswiri a league 2024 a Silver Strikers m’masewelo awo oyamba, ndipo Adepoju anasankhidwa kukhala osewera wa pamwamba pomwe waweluka ndi 100,000 Kwacha.

Advertisement