A Norman Chisale omwe ndi mtsogoleri wa achinyamata mu chipani cha Democratic Progressive (DPP), yemwenso ndi wachitetezo wamkulu wa a Peter Mutharika wati mtsogoleri wawo sadakule ndipo adakali ndi mphamvu mwakuti akhonza kutsogolera dziko.
A Chisale anayankhula izi ku Nyambadwe mu mzinda wa Blantyre, pamene akukonzekera kuyamba ulendo wa misonkhano yoyimayima yomwe akonza mu mzindawu. Iwo ati chiyambireni kuteteza a Mutharika sanauzidweko kuti adwala ngakhale poyenda amayenda ndi mphamvu kufika powaposa achinyamata ena.
Pa zakalata yofuna kuwamanga iwo ati sakadzipeleka okha ku polisi chifukwa sanalakwe kanthu ndipo ngati akuwafuna awayimbira telefoni kuti akufunika. Iwo anawonjezeranso kuti apolisi akhalanso akuwalondalonda mu mzinda wa Blantyre ndi Lilongwe zomwe anthu sakudziwa.
A Chisale atsindika kuti anthu akhulupilire kuti chipani cha DPP chikalowa m’boma moyo udzabwelera mchimake.
Iwo anatinso ngakhale ma dera ena akulembetsa ana, anawo adzasankha a Muntharika zomwe ndi zosadandaulitsa.
A Mutharika akuyembekezeka kuchititsa misonkhano yoyimayima ma dela monga; Chemusa, Chirimba, Kameza roundabout, Luwanda, Khama, Makhetha, Ndirande, Manje ndi Bangwe Mvula.