Atalankhula modzifutukula ku nyumba yawo ya boma ku Mudi mu mzinda wa Blantyre nkumati chomwe akufuna a UTM achite mwansanga chifukwa atopa ndi kumangowazungulira m’mbali, a Michael Usi tsopano mawu awo aphera mphongo pamene awachotsa mchipani mwachangu patangodutsa maola ochepa komiti yosungitsa mwambo itawayitana.
A Usi omwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino dzulo sanapite kukawonekera ku komiti yosungitsa mwambo yomwe inawayitana ku Lilongwe ndipo m’malo mwake iwo anali kumudzi kwawo ku Mulanje kukagawa ufa.
A Usi lamulungu anapeleka chitsanzo cha M’baibulo kuti Yesu anauza Yudasi kuti, ‘Yudasi chomwe ukufuna kupangacho panga mwachangu, nde nanenso ndiauze kuti chomwe mukufuna kupangacho pangani mwachangu chifukwa ndikudziwa chomwe mukufuna,’ anatelo a Usi.
Malinga ndi kalata yomwe UTM yatulutsa yomwe watsimikiza ndi mkulu ofalitsa nkhani ku UTM, a Felix Njawala ati chipanichi chawachotsa a Usi chifukwa amabweretsa migawano mchipani komanso kusokoneza otsatira ndinso kuvomeleza MCP kuti ndicho chipani chomwe chitenge boma zomwe ndi zosemphana ndi malamulo a chipanichi
A Usi lamulungu anati iwo sangakakhale pansi kumazengedwa kulakwa ndi komiti yomwe ati inasankhidwa mosatsata malamulo ku nsonkhano wake waukulu m’mwezi wa Novembala.
A Katswiri ena a ndale ati a Usi akukhala ndi otsatira ndipo zonse zikuwoneka zabwino chifukwa adakali mkhwapa mwa boma kutsatira mpando wawo wa wachiwiri kwa mtsogoleri koma anati zomwe zachitikira a Usi ndi zowononga mbiri yawo pa ndale komanso tsogolo lawo pa ndale.