
Anthu ambiri m’masamba anchezo akuthera mawu mphunzitsi wa timu ya miyendo ya dziko lino ya Flames, Calisto Pasuwa kamba kosiya osewera ena pa mndandanda wa omwe akuyenera kutenga gawo pa masewero odzipezera malo mu mpikisano wa dziko lonse (World Cup) masiku akudzawa.
Ena mwa osewera odziwika bwino omwe Pasuwa sanawaitane ndi monga Binwell Katinji yemwe anamwetsa zigoli ziwiri pa masewero omwe Flames idasewera ndi Comoros, Chimwemwe Idana, Stanley Sanudi, Uchizi Vunga komaso Isaac Kaliati kungotchulapo ochepa chabe.
Anthu ambiri omwe ayikira ndemanga pa mndandanda wa osewerawa akudzudzula Pasuwa ponena kuti ena mwa osewera omwe waitana ndi mphwemphwa kuyeleka ndi michonya ina yomwe wayisiya.
“Chimwemwe Idana, Stanley Sanudi, Chifundo Mphasi, Ali kuti? Nde mpaka kusiya Katinji nkutenga Kondowe, aaa koma ntchito mukuifuna?” wadabwa munthu wina yemwe adaikira ndemanga pa tsamba lino za mndandanda wa osewerawa.
Anthu ena adzudzulaso Pasuwa kuti watenga osewera ambiri ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets yomwe amaphunzitsa kale. “Ingonenani kuti iyi ndi Bullets Silver FC osati Flames isaa,” watelo wina poyikira ndemanga pa tsamba la fesibuku la FAM.
Pa mndandanda wa osewera 28, Pasuwa watenga osewera 8 kuchokera ku timu ya Bullets, 6 ku Silver Strikers, awiri ku Mighty Wanderers, pomwe 11 ndi osewera mayiko akunja komaso John Banda yemwe alibe timu pano. Mwa osewera 11 akunja omwe ayitanidwa, 5 anali osewera a timu ya Bullets sizoni yapitayi.
Komabe, anthu ena ayikira kumbuyo Pasuwa ponena kuti mphunzitsiyu akuyenera kuyika pa mndandanda osewera omwe akuwona kuti amuthandiza kupeza zotsatira zabwino pomwe Flames ikhale ikukumana ndi timu ya Namibia komaso Tunisia.