Za chipanizi nthawi zina kumaziona bwino – Usi

Advertisement
Usi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wakale wa UTM Micheal Usi walangiza anthu kuti adzikhala mwa mtendere ndi anzawo ndipo adzigwiritsa ntchito mutu wawo potsatira zipani ponena kuti asamangolonda komwe anzawo apita mosaganizira bwino.

A Usi alankhula izi kumudzi kwawo kwa Ngolowera mfumu yayikulu Chikumbu m’boma la Mulanje lero komwe anapita kukagawira anthu a dera la kwawo ufa wa nsima wa m’mapekete, feteleza komanso mbewu.

Mkulankhula kwawo, a Usi alimbikitsa anthu kuti adzikhalirana bwino wina ndi nzake ndipo zipani za ndale zisalekanitse anthu.

“Za ndalezi nthawi zina kumaziona bwino, ena amangokhala ngati chithangasala kuti ena akangoti apita uku nawo konko, ena akalowera uko nanu konko, zimafunika kuti aliyense azigwiritsa ntchito mutu wake kuganiza,” anatero a Usi.

Mtsogoleri wakale wa UTM yu wati nzosabisa kuti mdziko muno muli njala ya dzawoneni kotero nkofunika kuganizira anthu amene alibe chakudya. Iwo anatinso ufa agawawu ndi kudzera mu kusaka kwaokha koma anadziwitsa a Chakwera za ulendo wawowu.

A Estery Wyson a m’mudzi omwewu wa Ngolowera ati ndi okondwa ndi zomwe a Usi achita ponena kuti sanayembekezere kulandira feteleza komanso ufa, iwo anati mwana wa eni ukamulera bwino umadya nayedi.

A Ellen Suwedi anati chimwemwe chawo nchochuluka pakulandira nawo chakudya.

A Usi agwiritsa ntchito tsiku la lero lomwe iwo amayenera kukawonekera ku komiti yosungitsa mwambo ya chipani cha UTM mu mzinda wa Lilongwe. A Usi anakana kukawonekera ku komitiyo ponena kuti komitiyo idasankhidwa mosatsata malamulo ku nsonkhano wake waukulu mu November ndipo a Usi dzulo anatsogoza mawu odziphera mphongo kuti chomwe akufuna a UTM apange poti akuchedwa nkuwazungulira m’bali.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.