Chakwera ayikira kumbuyo mitengo yokwera ya Feteleza

Advertisement
Lazarus Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati akudziwa kuti feteleza anthu akugura pa mtengo wa K105 thousand pa thumba la 50kg, ndipo ati ngakhale zili choncho alimi akukwanitsabe kugura thumbali akangogulitsa matumba awiri okha achimanga kusiyana ndi kale pomwe amatha kugulitsa matumba asanu (5) kuti agule thumba.

Phungu wa dera la kumpoto cha ku madzulo kwa boma la Nkhatabay a Julius Mwase Phiri anafunsa a Chakwera mnyumba ya Malamulo lero ngati akudziwa kuti anthu akugura feteleza ndalama zopitilira 105 thousand kwacha pa thumba zomwe ndi zosiyana ndi zomwe analonjeza pokopa anthu kuti adzagura thumba pa mtengo wa K4495.

Mkuyankha kwawo a Chakwera anati mitengo ya zokolora za alimi yakhara ikukwera chaka ndi chaka akamagulitsa ndipo ati nkhani ya kukwera mitengo kwa zinthu isamayang’anidwe mbali imodzi.

Iwo anati nzosabisa kuti mitengo ya zinthu pa dziko lapansi sinakhazikike koma ayesetsabe kukhazikika pa mtengo wa k15,000 pa thumba la feteleza wa AIP ngakhale mitengo yake yakwera kangapo.

Iwo anati ndi chinthu choopsya kumayembekezera kuti mitengo ya zinthu ikhala chimodzimodzi pamene aliyense sanathe kuona ndikuyembekezera mavuto amene dziko ladutsamo.

A Chakwera anatsindika kuti kwakukulu kofunika ndi kulimbikitsa alimi powagura mbeu zawo pa mitengo yabwino, ndipo ati pano ali pa dongosolo loti ma kampane ochokera mdziko la Morrocco ayambitse ntchito yopanga feteleza pamwamba pa kampani yomwe ilipo kale kuno ku Malawi.

Pamene nyumba ya malamulo ikumaliza zokambirana zake lachisanu sabata ino, a Chakwera lero anakaonekera ku nyumba ya malamulo monga mwa m’mene amafunira malamulo adziko lino ndipo ayankha mafunso akulu akulu anayi mwa mafunso asanu amene anali pa mndandanda wa zokambirana lero.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.