Malo olembetsera kalembera wachisankho mulibe zipangizo za NRB m’boma la Zomba

Advertisement
Zomba

Pamene ndime yachiwiri yakelembera wachisankho yatsala masiku khumi kuti ithe m’boma la Zomba, zadziwika kuti malo omwe kalembelayu akuchitikira mulibe zipangizo za Bungwe lomwe limalemba ziphatso za unzika la National Registration Bureau (NRB).

Nzika zokhudzidwa zomwe zilibe ziphaso za unzika koma zidapita kuti zikalembetse zatiuza kuti zakhala zikubwezedwa kumalo olembetserawa popeza zipangizo za NRB kulibe.

Poyankhulapo zokulephera kugwira ntchito kwa Bungwe lomwe limalemba ziphatso za unzika (NRB) Mfumu ya Mzinda wa Zomba Khansala Christopher Jana wati alindi nkhawa kuti anthu ambiri sadzaponya nawo voti pachisankho cha chaka chamawa. 

Khansala Jana wati zomwe likuchita Bungwe lomwe limalemba ziphaso za unzika la NRB polephera kulemba anthu omwe alibe chiphatso ndikuphwanya ufulu wawo oti adzavote pachisankho chosankha mtsogoleri wa dziko, aphungu akunyumba yamalamulo komanso makhansala cha 2025 ndipo wapempha bungwe lowoona zachisankho kuti liwonjezere masiku popeza masiku anayi oyambilira anthu ambiri sadalembetse.

Poyankhulaponso za vutoli, Khansala wam’dera la Likangala Monira Bakali wati ndizomvetsa chisoni kuti ngakhale anthu omwe alibe chiphaso cha unzika koma adalembetsa mukawundula ndipo adapatsidwa mapepala osonyeza kuti adalembetsa akumabwedzedwabe kumalo olembetsera kalembera wachisankho.

Khansala Bakali wati izi ndizokhumudwitsa kwambiri kumtundu wa a Malawi popeza ufulu woponya voti ndiwa aliyense yemwe wakwanitsa zaka 18 zakubadwa

Malawi24 idayesera kuti ilankhule ndi Mkulu wa Bungwe la NRB a Mphatso Sambo pomwe imalemba nkhaniyi koma lamiya yawo yammanja simapezeka.

Bungwe lowona zachisankho la MEC lidayamba gawo lachiwiri lakalembera m’bomali Loweruka pa 9 November ndipo likembekezereka kudzatsiliza kalembelayu pa 22 November.

Advertisement