Vuto lakusowa kwa madzi lakula m’boma la Ntchisi

Advertisement
Ntchisi

Anthu okhala m’mudzi wa Chikho, Mfumu yayikulu Kasakula m’boma la Ntchisi adanduala za vuto la madzi lomwe lakula m’mudziwu. Mudzi wa Chikho mulibe dilawo komanso mpope, ndipo anthu okhala mudziwu amakatunga madzi ochoka mu phiri omwe siwotetezeka.

Anthuwa amayenda mtunda wawutali kuchoka mudzi omwe amakhala kupita kunseli kwa phiri lomwe linazungulira mudziwu kuti akatunge madziwa. Akatunga madziwa anthuwa amakwela chitunda chachikulu kuti afike manyumba awo.

Polakhula ndi Malawi24, Mayi Ellen a mudziwu, anati akukhala movutika chifukwa cha vuto la madzili ndipo akufuna chithandizo cha dilawo kapena mpopi.

Iwo anapitiliza kunena kuti amavutika mayendedwe chifukwa akasenza ndowa ya madzi kuchoka kuseli kwa phiri, amavutika kuti akwele chitunda chomwe ndichachikulu kwambiri.

“Tikukhala movutika kwambiri, madziwa timatunga inde Koma movutika ndipo madziwaso ndi wosatetezeka moti nthawi zina timadwala matenda otsegula m’mimba.

“Komanso mayendedwe ndiwovuta moti chaka chatha ndinatchoka mwendo chifukwa chachitunda chomwe timakwera tikanyamula madziwa. Ana amapitaso ku sukulu mochedwa pena amapita osasamba chifukwa kuti tifike kuno kuzatunga madzi ndi nthawi yambiri,” Iwo anatero.

Polakhulapo, a Senior Group Kandodo 2 anati anthu a m’mudziwu akukhala movutika kwambiri chifukwa madzi ndi moyo, ndipo madzi akakhala kuti akusowa kapena akuvuta mapezedwe ake moyo wake umakhala wa penda penda.

Iwo anapempha Boma komanso mabungwe kuti awathandize ndi dilawo kapena mpopi chifukwa zinthu sizilibwino.

M’mudzi wa chikhowu muli mawanja osachepela 262, ndipo sadakhalepo ndi dilawo chiyambileni ndipo ati atopa ndi kumwa madzi opanda ukhondo.

Bungwe la Water Aid lanena kuti pompano akhale akubweletsera dilawo m’mudzi wa Chikho kuti achepetse vuto la kusowa kwa madzi.

Mkulu owona za ma program mu project ya madzi ndi ukhondo kubugwe la water Aid a Laston Zulu ndiwo ananena izi, ndipo anatsimikizira anthu okhala mudziwu kuti kumapeto kwa mwezi uno ayamba ntchito yoika mjigowo.

Malinga ndi a Zulu ndalama zosachepela 12 million kwacha ndi zomwe agwiritse ntchito pa ntchitoyo.

Advertisement