Ukayipa dziwa nyimbo: Mavenda ndiwo akupangitsa kuti mafuta asowe – a Kachaje

Advertisement
Malawian scramble for fuel

Mkulu wa bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA), Henry Kachaje wati mavenda omwe akumagulisa mafuta mosavomerezeka pa misika yachinyengo ndi amene akupangisa kuti mafuta azipitililabe kusowa m’dziko muno. 

A Kachaje anena izi lachiwili pomwe anawokenera ku komiti yaku nyumba yamalamulo yoona zamafakitale, malonda ndi zokopa alendo mu mzinda wa Lilongwe komwe amakafotokoza zomwe bungweli likuchita pofuna kuthana ndi vuto lakusowa kwa mafuta lomwe lafika pa mwana wakana phala. 

Iwo aloza chala mavendawa kuti ndiwo akukolezera vutoli ponena kuti akumagula mafuta ochuluka m’malo omwetsera mafuta ndikumawagulisa pa mitengo yokwera ‘misika yachingengo zomwe zikupangisa kuti mafuta azisowabe m’dziko muno. 

A Kachaje anaonjezera ndinena kuti mafuta omwe anabwera m’dziko muno sabata latha anali okwanira kuthana ndi vuto lakosowa kwamafuta koma mpaka pano vutoli silikutha kamba kamavendawa. 

Patha ma sabata atatu tsopano mafuta agalimoto akupitililabe kusowa zomwe zasokoneza ntchito zosiyanasiyana m’dziko muno. 

Advertisement