Mtetemera wayimitsidwanso ntchito ku Creck Sporting

Advertisement
MacDonald Mtetemera

Ikakuona litsiro siikata! Patangotha mwezi umodzi atabwezeretsedwa paudindo womwe adayimitsidwa, mphunzitsi wamkuku wa timu ya Creck Sporting, Macdonald Nginde Mtetemera waimitsidwaso.

Timu ya Check Sporting yalengeza za kuimitsidwa kwa Mtetemela Lachiwiri pa 29 October 2024, chiganizo chomwe yati yapanga kutsatira kusachita bwino kwa timuyi m’masewero ake angapo apitawa.

Mlembi wamkulu watimuyi a Aaron Mtaya watsimikizira nyumba zina zofalitsa nkhani m’dziko muno kuti; “Eya ndi zoona mphunzitsiyu wayimitsidwadi pa ntchito yake nkhani yake ndi yomwe ija yakusachita bwino kwa timuyi.”

Izi zikubwera kutsatira kugonja kwa timuyi pomwe imasewera ndi timu ya Karonga United ndi chigoli chimodzi kwa duu Lamulungu lapitali muchikho cha TNM.

M’mwezi wa July chaka chino, timu ya Creck Sporting idayimitsaso pa ntchito Nginde potsatiraso kusachita bwino kwa timuyi koma anabwezeretsedwaso pa 9 September 2024.

Padakali pano timuyi yomwe ili panambala 10 ndi ma poyitsi 32 pa masewero 23 omwe yasewera, ikhala ikutsogoleledwa ndi Joseph Kamwendo yemwe anali wachiwiri kwa Mtetemera.

Lero Lachitatu, timu ya Creck ikhala ikukumana ndi timu ya Civil Service United pa bwalo la Champion mu ligi ya TNM. 

Advertisement