Oweluza milandu Chief Resident Magistrate Rodrick Michongwe wapereka belo kwa Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM.
A Michongwe akana pempho la oyimira boma pa mlanduwu omwe amafuna kusungabe a Kaliati Kwa masiku asanu ndi awiri Ku Polisi pofuna kumalizitsa kafukufuku wawo.
Popereka chigamulo, a Michongwe anati oyimira boma pa mlanduwu akudzitsutsa okha pamene akunena kuti akatswiri ofufuza anafufuza mlanduwu asanamange Kaliati koma iwo omwewo akupemphanso kuti apatsidwe nthawi yofufuza.
Malinga ndi a Michongwe, boma likanadikira masiku asanu ndi awiri omwe akupemphawa kumaliza kaye kafukufuku asanamange oyimbidwa mlanduwa.
Michongwe wati ambali yaboma sanapeleke zifukwa zokwanira zokhudza kusungabe Kaliati kaamba kakuti ma phone onse a oganizilidwawa ali mmanja mwa boma ndipo ali ndi mwayi opeza zonse zomwe akufuna.
Malingana ndi ozenga mlanduyu ambali yaboma akuti akuopa kuti a Kaliati akasokoneza mboni zaboma ndikuti ambali yaboma malingana ndi malamulo amayenera aonetse chiopsyezo chomwe chilipo atamutulutsa oyimbidwa mlandu zomwe sizinachitike.
Iye wati palibe umboni wina ulionse osonyeza kuti kunali kafukufuku lisanafike tsiku lachinayi sabata lathali.
A Michongwe alamula a Kaliati kupereka ndalama yokwana 1 Million kwacha kuphatikizapo 500,000 kwacha ngati chikole.
Iwowa alamulaso a Kaliati Kuti azikawonekela Ku likulu la a Police pakatha masabata awiri.
A Kaliati awalamulaso Kuti asiye zikalata zoyendela (passport) komanso asasokoneze umboni uliwonse pa nkhaniyi.
Mayi Patricia Kaliati anawamanga lachinayi sabata latha pa mulandu omwe akuti akuwaganizira kuti amapanga upo ndi azawo ena awiri ofuna kupha m’tsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.